1 Mas. 148.13 Yehova, Ambuye wathu,
dzina lanu liposadi nanga padziko lonse lapansi!
Inu amene munaika ulemerero wanu pa thambo la kumwamba.
2 Mat. 21.16 M'kamwa mwa makanda ndi oyamwa munakhazikitsa mphamvu,
chifukwa cha otsutsana ndi Inu,
kuti muwaletse mdani ndi wobwezera chilango.
3 Mas. 19.1 Pakuona ine thambo la kumwamba lanu, ntchito ya zala zanu,
mwezi ndi nyenyezi, zimene munazikhazika,
4 Mas. 144.3; Aheb. 2.6 munthu ndani kuti mumkumbukira?
Ndi mwana wa munthu kuti mucheza naye?
5Pakuti munamchepsa pang'ono ndi Mulungu,
munamveka iye korona wa ulemerero ndi ulemu.
6 Gen. 1.26, 28; 1Ako. 15.27 Munamchititsa ufumu pa ntchito za manja anu;
mudagonjetsa zonse pansi pa mapazi ake;
7nkhosa ndi ng'ombe, zonsezo,
ndi nyama zakuthengo zomwe;
8mbalame za m'mlengalenga, ndi nsomba za m'nyanja.
Zopita m'njira za m'nyanja.
9Yehova, Ambuye wathu,
dzina lanu liposadi nanga padziko lonse lapansi!
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.