AMOSI Mau Oyamba - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

Mau OyambaAmosi anali mneneri woyamba amene uthenga wake unalembedwa pafupifupi wonse. Ngakhale amachokera ku Yuda, iye analalikira kwa anthu a mu ufumu wa kumpoto kwa Israele m'zaka za pafupifupi 750 BC. Iyi inali nthawi imeneyo dziko linali pa mtendere, ndipo zinthu zimayenda bwino kumbali ya chuma komanso anthu amakonda kupembedza. Komabe Amosi adaona kuti odyerera chuma anali olemera okha basi, ndipo iwo amagwiritsa ntchito mphamvu zawo pofuna kupondereza osauka. Kupembedza kwao kunali kwachinyengo ndipo chitetezo sichinali monga zinthu zimaonekera. Analalikira ndi mtima wake wonse komanso mwamphamvu kuti Mulungu adzaononga dzikolo. Iye anawadandaulira kuti chilungamo chiyende “ngati mtsinje wosefuka” (5.24), ndi kuti pakutero, “kapena Yehova Mulungu wa makamu adzachitira chifundo otsala a Yosefe.” (5.15)Za mkatimuChiweruzo pa maiko oyandikana ndi Israele 1.1—2.5

Chiweruzo pa Israele 2.6—6.14

Masomphenya asanu 7.1—9.15

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help