MASALIMO 104 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

Ulemerero wa Mulungu m'zolengedwa ndi m'kuzisunga komwe

1Lemekeza Yehova, moyo wanga;

Yehova, Mulungu wanga, Inu ndinu wamkulukulu;

2 Mas. 93.1; Dan. 7.9 muvala ulemu ndi chifumu.

Amene mudzikuta nako kuunika monga ndi chovala;

ndi kuyala thambo ngati nsalu yotchinga.

3 Yes. 19.1 Amene alumikiza mitanda ya zipinda zake m'madzi;

naika makongwa akhale agaleta ake;

nayenda pa mapiko a mphepo.

4 Aheb. 1.7 Amene ayesa mphepo amithenga ake;

lawi la moto atumiki ake;

5anakhazika dziko lapansi pa maziko ake,

silidzagwedezeka kunthawi yonse.

6 Gen. 7.19 Mudalikuta ndi nyanja ngati ndi chovala;

madzi anafikira pamwamba pa mapiri.

7Pa kudzudzula kwanu anathawa;

anathawa msanga liu la bingu lanu;

8anakwera m'mapiri, anatsikira m'zigwa,

kufikira malo mudawakonzeratu.

9Munaika malire kuti asapitirireko;

kuti asabwererenso kuphimba dziko lapansi.

10Atumiza akasupe alowe m'makwawa;

ayenda pakati pa mapiri:

11Zimamwamo nyama zonse zakuthengo;

mbidzi zipherako ludzu lao.

12Mbalame za mlengalenga zifatsa pamenepo,

zimaimba pakati pa mitawi.

13 Mas. 147.8 Iye amwetsa mapiri mochokera m'zipinda zake:

Dziko lakhuta zipatso za ntchito zanu.

14 Gen. 1.29-30 Ameretsa msipu ziudye ng'ombe,

ndi zitsamba achite nazo munthu;

natulutse chakudya chochokera m'nthaka;

15ndi vinyo wokondweretsa mtima wa munthu,

ndi mafuta akunyezimiritsa nkhope yake,

ndi mkate wakulimbitsa mtima wa munthu.

16Mitengo ya Yehova yadzala ndi madzi;

mikungudza ya ku Lebanoni imene anaioka;

17m'mwemo mbalame zimanga zisa zao;

pokhala chumba mpa mitengo ya mikungudza.

18Mapiri aatali ndiwo ayenera zinkhoma;

pamatanthwe mpothawirapo mbira.

19Anaika mwezi nyengo zake;

dzuwa lidziwa polowera pake.

20Muika mdima ndipo pali usiku;

pamenepo zituluka zilombo zonse za m'thengo.

21Misona ya mkango ibangula potsata nyama yao,

nifuna chakudya chao kwa Mulungu.

22Potuluka dzuwa, zithawa,

zigona pansi m'ngaka mwao.

23Pamenepo munthu atulukira kuntchito yake,

nagwiritsa kufikira madzulo.

24 Mas. 8.3; Miy. 3.19 Ntchito zanu zichulukadi, Yehova!

Munazichita zonse mwanzeru;

dziko lapansi lidzala nacho chuma chanu.

25Nyanja siyo, yaikulu ndi yachitando,

m'mwemo muli zokwawa zosawerengeka;

zamoyo zazing'ono ndi zazikulu.

26M'mwemo muyenda zombo;

ndi Leviyatani amene munamlenga aseweremo.

27 Mas. 145.15 Izi zonse zikulindirirani,

muzipatse chakudya chao pa nyengo yake.

28Chimene muzipatsa zigwira;

mufumbatula dzanja lanu, zikhuta zabwino.

29 Mlal. 12.7 Mukabisa nkhope yanu, ziopsedwa;

mukalanda mpweya wao, zikufa,

ndipo zibwerera kufumbi kwao.

30 Gen. 1.1-2; Yes. 32.15 Potumizira mzimu wanu, zilengedwa;

ndipo mukonzanso nkhope ya dziko lapansi.

31 Gen. 1.31 Ulemerero wa Yehova ukhale kosatha;

Yehova akondwere mu ntchito zake;

32amene apenyerera padziko lapansi, ndipo linjenjemera;

akhudza mapiri, ndipo afuka.

33 Mas. 63.4 Ndidzaimbira Yehova m'moyo mwanga:

ndidzaimbira Mulungu wanga zomlemekeza pokhala ndilipo.

34Pomlingirira Iye pandikonde;

ndidzakondwera mwa Yehova.

35 Miy. 2.22 Ochimwa athedwe kudziko lapansi,

ndi oipa asakhalenso.

Yamika Yehova, moyo wanga.

Aleluya.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help