1Mzimu wanga watha, masiku anga afafanizika,
kumanda kwandikonzekeratu.
2Zoonadi, ali nane ondiseka;
ndi diso langa lili chipenyere m'kundiwindula kwao.
3 Miy. 6.1; 17.18 Mupatse chigwiriro tsono,
mundikhalire chikole Inu nokha kwanu;
ndani adzapangana nane kundilipirira?
4Pakuti mwabisira mtima wao nzeru;
chifukwa chake simudzawakuza.
5Iye wakupereka mabwenzi ake ku ukapolo,
m'maso mwa ana ake mudzada.
6Anandiyesanso chitonzo cha anthu;
ndipo ndakhala ngati munthu womthira malovu pankhope pake.
7 Mas. 6.7 M'diso mwanga muchita chizirezire chifukwa cha chisoni,
ndi ziwalo zanga zonse zilibe chithunzi.
8Anthu oongoka mtima adzadabwa nacho,
ndi munthu wosalakwa adzadziutsa kumtsutsa wonyoza Mulunguyo.
9 Mas. 24.4 Koma wolungama asungitsa njira yake,
ndi iye wa manja oyera adzakulabe mumphamvu.
10Koma bwerani inu nonse, idzani tsono;
pakuti sindipeza mwa inu wanzeru.
11Masiku anga apitirira, zolingirira zanga zaduka,
zakezake zomwe za mtima wanga.
12Zisanduliza usiku ukhale usana;
kuunika kuyandikana ndi mdima.
13Ndikayembekezera kumanda kukhale nyumba yanga;
ndikayala pogona panga mumdima.
14Ndikati kwa dzenje, Ndiwe atate wanga;
kwa mphutsi, Ndiwe mai wanga ndi mlongo wanga;
15chilikuti chiyembekezo changa?
Inde, chiyembekezo changa adzachiona ndani?
16Chidzatsikira kumipingiridzo ya kumanda,
pamene tipumulira pamodzi kufumbi.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.