YESAYA 52 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

1 Yes. 51.9, 17; Nah. 1.15 Galamuka! Galamuka! Tavala mphamvu zako, Ziyoni; tavala zovala zako zokongola, Yerusalemu, mzinda wopatulika; pakuti kuyambira tsopano sadzalowanso kwa iwe wosadulidwa ndi wodetsedwa.

2Dzisanse fumbi; uka, khala tsonga, Yerusalemu; udzimasulire maunyolo a pakhosi pako, iwe mwana wamkazi wam'nsinga wa Ziyoni.

3 Mas. 44.12 Pakuti atero Yehova, Inu munagulitsidwa chabe, ndipo mudzaomboledwa opanda ndalama.

4Gen. 46.6; Mac. 7.14-15Pakuti Ambuye Yehova atero, Anthu anga ananka ku Ejipito poyamba paja, kukakhala kumeneko; ndipo Asiriya anawatsendereza popanda chifukwa.

5Ezk. 36.20, 23; Aro. 2.24Chifukwa chake kodi ndichitenji pano? Ati Yehova; popeza anthu anga achotsedwa popanda kanthu? Akuwalamulira awaliritsa, ati Yehova; ndipo dzina langa lichitidwa mwano tsiku lonse kosalekeza.

6Chifukwa chake anthu anga adzadziwa dzina langa; chifukwa chake tsiku limenelo iwo adzadziwa kuti Ine ndine amene ndinena; taonani, ndine pano.

7 Nah. 1.15 Ha, akongolatu pamapiri mapazi a iye amene adza ndi uthenga wabwino, amene abukitsa mtendere, amene adza ndi uthenga wabwino wa zinthu zabwino, amene abukitsa chipulumutso; amene ati kwa Ziyoni, Mulungu wako ndi mfumu.

8Mau a alonda ako! Akweza mau, aimba pamodzi; pakuti adzaona maso ndi maso, pamene Yehova abwerera kudza ku Ziyoni.

9Yes. 48.20; 51.3Kondwani zolimba, imbani pamodzi, inu malo abwinja a pa Yerusalemu; pakuti Yehova watonthoza mtima wa anthu ake, waombola Yerusalemu.

10Mas. 98.1-3; Mat. 26.63; 27.12, 14Yehova wavula mkono wake woyera pamaso pa amitundu onse; ndi malekezero onse a dziko lapansi adzaona chipulumutso cha Mulungu wathu.

11Lev. 22.1-33; Yer. 51.6, 45; 2Ako. 6.17Chokani inu, chokani inu, tulukani ku Babiloni; musakhudze kanthu kodetsa; tulukani pakati pake, khalani okonzeka, inu amene munyamula zotengera za Yehova.

12Eks. 14.19Pakuti simudzachoka mofulumira, kapena kunka mothawa; pakuti Yehova adzakutsogolerani, ndi Mulungu wa Israele adzadikira pambuyo panu.

13 Yer. 23.5; Afi. 2.9 Taonani, Mtumiki wanga adzachita mwanzeru; adzakwezedwa ndi kutukulidwa pamwamba, nadzakhala pamwambamwamba.

14Mas. 22.6-7; Yes. 53.2-3Monga ambiri anazizwa ndi iwe Israele, momwemo nkhope yake yaipitsidwa ndithu, kupambana munthu aliyense, ndi maonekedwe ake kupambana ana a anthu;

15Ezk. 36.25; Aro. 15.21; Aheb. 9.13-14momwemonso Iye adzawazawaza mitundu yambiri; mafumu adzamtsekera Iye pakamwa pao; pakuti chimene sichinauzidwe kwa iwo adzachiona, ndi chimene iwo sanamve adzazindikira.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help