YEREMIYA Mau Oyamba - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu
Mau OyambaMneneri Yeremiya adalalikira kwa zaka zambiri, mzinda wa Yerusalemu usanapasuke (586 BC), ndiponso zaka zina zingapo mzindawo utapasuka. Mau ake ambiri ngochenjeza Ayuda akuti likubwera tsiku pamene Mulungu adzawalanga ndi kuwononga Yerusalemu, chifukwa cha machimo ao ndi kupembedza milungu ina. Tsono zimenezi zidachitikadi pamene Nebukadinezara mfumu ya Babiloni adadzazinga mzindawo nkuwuononga pamodzi ndi Kachisi wa Yehova; anthu ake ambiri pamodzi ndi mfumu yomwe adawatenga ukapolo nkupita nawo ku Babiloni, Yeremiya uja akuwona. Iye adalankhulanso mau ena onena kuti tsiku lina anthu otengedwa ku ukapolowo adzabwerera kwao ndi kukhalanso pabwino.Yeremiya anali munthu wachifundo, wokonda Ayuda anzake kwambiri; ankawamvera chisoni ndipo nchifukwa chake ankayenera kuwadzudzula ndi kuwachenjeza. Mau ake aonetsa kuti ntchito imene Yehova adamupatsa inkawawitsa mtima wake. Mau a Yehova ankayaka ngati moto mumtima mwake, kotero kuti sankathanso kusunga mauwo mumtima mwake mpaka atalengeza zonse.Mau ena a m'bukuli aloza zakutsogolo pamene Yehova adzakhazika chipangano chatsopano, cholembedwa m'mitima ya anthu, mwakuti anthuwo sadzasowanso mphunzitsi wowakumbutsa zimenezi (31.31-34).Za mkatimuBukuli lili ndi zigawo zingapo:Kuitanidwa kwa Yeremiya 1.1-19 Mau a Yehova kwa atsogoleri ao 2.1—25.38Mau ena a Yehova ndipo zochitika zina ndi zina 26.1—45.5Mau ena otsutsa mitundu ina ya anthu 46.1—51.64Mau oonjezera osimba za kupasuka kwa mzinda wa Yerusalemu 52.1-34