1 Mas. 92.1 Aleluya; Pakuti kuimbira zomlemekeza Mulungu wathu nkokoma;
pakuti chikondweretsa ichi, chilemekezo chiyenera.
2 Deut. 30.3; Yes. 11.12 Yehova amanga Yerusalemu;
asokolotsa otayika a Israele.
3 Yes. 57.15; 61.1 Achiritsa osweka mtima,
namanga mabala ao.
4 Yes. 40.26 Awerenga nyenyezi momwe zili;
azitcha maina zonsezi.
5 Yes. 40.28 Ambuye wathu ndi wamkulu ndi wa mphamvu zambiri;
nzeru yake njosatha.
6 Mas. 146.8-9 Yehova agwiriziza ofatsa;
atsitsira oipa pansi.
7Yamikani Yehova ndi kuthira mang'ombe;
muimbireni Mulungu wathu zomlemekeza pazeze:
8Amene aphimba thambo ndi mitambo,
amene akonzera mvula nthaka,
amene aphukitsa msipu pamapiri.
9 Mas. 145.15; Mat. 6.26 Amene apatsa zoweta chakudya chao,
ana a khwangwala alikulira.
10 Hos. 1.7 Mphamvu ya kavalo siimkonda:
Sakondwera nayo miyendo ya munthu.
11Yehova akondwera nao akumuopa Iye,
iwo akuyembekeza chifundo chake.
12Yerusalemu, lemekezani Yehova;
Ziyoni, lemekezani Mulungu wanu.
13Popeza analimbitsa mipiringidzo ya zitseko zanu:
Anadalitsa ana anu m'kati mwanu.
14 Deut. 32.13-14; Yes. 60.17-18 Ndiye amene akhalitsa malire anu mumtendere;
akukhutitsani ndi tirigu wakucha bwino.
15Atumiza lamulo lake kudziko lapansi;
mau ake athamanga liwiro.
16Apatsa chipale chofewa ngati ubweya;
awaza chisanu ngati phulusa.
17Aponya matalala ake ngati zidutsu:
Adzaima ndani pa kuzizira kwake?
18Atumiza mau ake nazisungunula;
aombetsa mphepo yake, ayenda madzi ake.
19Aonetsa mau ake kwa Yakobo;
malemba ake, ndi maweruzo ake kwa Israele.
20 Aro. 3.1-2 Sanatero nao anthu a mtundu wina;
ndipo za maweruzo ake, sanawadziwe.
Aleluya.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.