NUMERI 24 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

1Pamene Balamu anaona kuti kudakomera pamaso pa Yehova kudalitsa Israele, sanamuke, monga nthawi zina zija, ku nyanga zolodzera, koma anayang'ana nkhope yake kuchipululu.

21Sam. 10.10Ndipo Balamu anakweza maso ake, naona Israele alikukhala monga mwa mafuko ao; ndipo mzimu wa Mulungu unadza pa iye.

3Pamenepo ananena fanizo lake, nati,

Balamu mwana wa Beori anenetsa,

ndi munthuyo anatsinzina maso anenetsa;

4 2Ako. 12.2 wakumva mau a Mulungu anenetsa,

wakuona masomphenya a Wamphamvuyonse,

wakugwa pansi maso ake openyuka.

5Ha? Mahema ako ngokoma, Yakobo;

zokhalamo zako, Israele!

6Ziyalika monga zigwa,

monga minda m'mphepete mwa nyanja,

monga khonje wooka Yehova,

monga mikungudza m'mphepete mwa madzi.

7Madzi adzayenda natuluka m'zotungira zake,

ndi mbeu zake zidzakhala ku madzi ambiri,

ndi mfumu yake idzamveka koposa Agagi,

ndi ufumu wake udzamveketsa.

8Mulungu amtulutsa mu Ejipito;

ali nayo mphamvu yonga ya njati;

adzawadya amitundu, ndiwo adani ake.

Nadzamphwanya mafupa ao,

ndi kuwapyoza ndi mivi yake.

9 Gen. 12.3 Anaunthama, nagona pansi ngati mkango,

ngati mkango waukazi; adzamuutsa ndani?

Wodalitsika aliyense wakudalitsa iwe,

wotemberereka aliyense wakutemberera iwe.

10Pamenepo Balaki anapsa mtima pa Balamu, naomba m'manja; ndipo Balaki anati kwa Balamu, Ndinakuitana kutemberera adani anga, ndipo unawadalitsa ndithu katatu tsopano.

11Chifukwa chake thawira ku malo ako tsopano; ndikadakuchitira ulemu waukulu; koma, taona, Yehova wakuletsera ulemu.

12Ndipo Balamu anati kwa Balaki, Kodi sindinauzanso amithenga anu amene munawatumiza kwa ine, ndi kuti,

13Chinkana Balaki akandipatsa nyumba yake yodzala ndi siliva ndi golide, sindikhoza kutumpha mau a Yehova, kuchita chokoma kapena choipa ine mwini wake; chonena Yehova ndicho ndidzanena ine?

14Mik. 6.5; Chiv. 2.14Ndipo tsopano, taonani, ndimuka kwa anthu a mtundu wanga; tiyeni, ndidzakulangizani, ndi kukuuzani zimene anthu awa adzachitira anthu anu, masiku otsiriza.

15Ndipo ananena fanizo lake, nati,

Balamu mwana wa Beori anenetsa,

ndi munthu wotsinzina masoyo anenetsa;

16anenetsa wakumva mau a Mulungu,

ndi kudziwa nzeru ya Wam'mwambamwamba,

wakuona masomphenya a Wamphamvuyonse,

wakugwa pansi wopenyuka maso.

17 Mas. 110.2; Mat. 2.2; Gen. 49.10 Ndimuona, koma tsopano ai;

ndimpenya, koma si pafupi ai;

idzatuluka nyenyezi mu Yakobo,

ndi ndodo yachifumu idzauka mu Israele,

nidzakantha malire a Mowabu,

nidzapasula ana onse a Seti.

18 2Sam. 8.14; Mas. 60.8 Ndi Edomu adzakhala akeake,

Seiri lomwe lidzakhala lakelake,

ndiwo adani ake;

koma Israele adzachita zamphamvu.

19 Gen. 49.10 Ndipo wina wotuluka mu Yakobo adzachita ufumu;

nadzapasula otsalira m'mizinda.

20 1Sam. 15.3, 8, 33 Ndipo anayang'ana ku Amaleke, nanena fanizo lake, nati,

Amaleke ndiye woyamba wa amitundu;

koma chitsiriziro chake,

adzaonongeka ku nthawi zonse.

21Ndipo anayang'ana Akeni, nanena fanizo lake, nati,

kwanu nkokhazikika,

wamanga chisa chako m'thanthwe.

22Koma Kaini adzaonongeka,

kufikira Asiriya adzakumanga nsinga.

23Ndipo ananena fanizo lake, nati,

Ha! Adzakhala ndi moyo ndani pakuchita ichi Mulungu?

24Koma zombo zidzafika kuchokera ku dooko la Kitimu,

ndipo adzasautsa Asiriya, nadzasautsa Eberi,

koma iyenso adzaonongeka.

25Ndipo Balamu anauka, namuka nabwerera kumalo kwake; ndi Balaki yemwe ananka njira yake.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help