2 MBIRI 16 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

Asa apangana ndi Benihadadi, nalimbana ndi Israele(1Maf. 15.17-22)

1 1Maf. 15.17-22 Chaka cha makumi atatu mphambu zisanu ndi chimodzi cha Asa, Baasa mfumu ya Israele anakwera kulimbana ndi Yuda, namangitsa Rama, kuwaletsa anthu asatuluke kapena kulowa kwa Asa mfumu ya Yuda.

2Pamenepo Asa anatulutsa siliva ndi golide ku chuma cha nyumba ya Yehova, ndi cha nyumba ya mfumu; nazitumiza kwa Benihadadi mfumu ya Aramu, yokhala ku Damasiko, ndi kuti,

3Pakhale pangano pakati pa ine ndi inu, monga pakati pa atate wanga ndi atate wanu; taonani, ndakutumizirani siliva ndi golide; mukani, pasulani pangano lanu ndi Baasa mfumu ya Israele, kuti andichokere.

4Ndipo Benihadadi anamvera mfumu Asa natumiza akazembe a magulu ake a nkhondo ayambane ndi mizinda ya Israele, nakantha Iyoni, ndi Dani, ndi Abele-Maimu, ndi mizinda yonse ya chuma ya Nafutali.

5Ndipo kunali, pakumva ichi Baasa, analeka kumangitsa Rama, naleketsa ntchito yake.

6Pamenepo Asa mfumu anatenga Ayuda onse, ndipo anatuta miyala ya ku Rama, ndi mitengo yake, imene Baasa adamanga nayo, namangira Geba ndi Mizipa.

Hanani mlauli adzudzula Asa

7 Yes. 31.1; Yer. 17.5 Nthawi yomweyi Hanani mlauli anadza kwa Asa mfumu ya Yuda, nanena naye, Popeza mwatama mfumu ya Aramu, osatama Yehova Mulungu wanu, chifukwa chake khamu la nkhondo la mfumu ya Aramu lapulumuka m'dzanja lanu.

82Mbi. 14.9, 12Nanga Akusi ndi Alibiya, sanakhale khamu lalikulukulu, ndi magaleta ndi apakavalo ambirimbiri, koma muja munatama Yehova anawapereka m'dzanja mwanu?

9Yer. 16.17Pakuti maso a Yehova ayang'ana uko ndi uko m'dziko lonse lapansi, kudzionetsera wamphamvu kwa iwo amene mtima wao uli wangwiro ndi Iye. Mwachita chopusa m'menemo; pakuti kuyambira tsopano mudzaona nkhondo.

10Mat. 14.3Koma Asa anakwiya naye mlauliyo, namuika m'kaidi; pakuti adapsa naye mtima chifukwa cha ichi. Nthawi yomweyi Asa anasautsa anthu ena.

11Ndipo taonani, zochita Asa, zoyamba ndi zotsiriza, zalembedwa m'buku la mafumu a Yuda ndi Israele.

12Yer. 17.5Ndipo Asa atakhala mfumu zaka makumi atatu mphambu zisanu ndi zitatu, anadwala nthenda ya mapazi, nikuladi nthendayi; koma podwala iye sanafune Yehova, koma asing'anga.

13Nagona Asa ndi makolo ake, namwalira atakhala mfumu zaka makumi anai.

14Gen. 50.2; Yer. 34.5; Mrk. 16.1Ndipo anamuika m'manda ake adadzisemerawo m'mzinda wa Davide, namgoneka pa kama wodzala ndi zonunkhira za mitundumitundu, monga mwa makonzedwe a osakaniza; ndipo anampserezera zopsereza zambiri.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help