MASALIMO Mau Oyamba - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

Mau OyambaIli ndi buku la nyimbo ndi mapemphero. Mau ake adalembedwa ndi anthu osiyanasiyana pa nthawi yaitali, ndipo Aisraele ankagwiritsa ntchito mauwo popembedza Yehova. Masalimowo alipo amitundumitundu: ena ndi nyimbo zotamanda Mulungu, zopembedza, kapena zothokoza; ena ndi mau opempha chithandizo ndi chitetezo pa nthawi ya mavuto, ena ndi mau olapa ndi opepesera machimo, mau opempha chikhululukiro, mwinanso mau opempha Mulungu kuti alange adani. Masalimowo ngothandiza anthu pakupemphera, aliyense molingana ndi zimene zadzaza mumtima wake, komanso moganizira zosowa za anthu onse a Mulungu ndi ubwino wao. Yesu nayenso ankagwiritsa ntchito Masalimowo popemphera; ndipo kuyambira pa chiyambi cha Mpingo, Akhristu akhala akugwiritsa ntchito buku lomwelo pamwambo wachipembedzo.Za mkatimuBukuli lili ndi zigawo zisanu:Masalimo 1 mpaka 41Masalimo 42 mpaka 72Masalimo 73 mpaka 89Masalimo 90 mpaka 106Masalimo 107 mpaka 150
Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help