1 Eks. 25.10; 34.1-2 Masiku aja Yehova anati kwa ine, Dzisemere magome awiri amiyala onga oyamba aja, nukwere kuno kwa Ine m'phiri umu, nudzipangire likasa lamtengo.
2Eks. 25.16Ndipo ndidzalembera pa magomewo mauwo anali pa magome oyamba aja amene unawaswa, ndipo uwaike m'likasamo.
3Potero ndinapanga likasa la mtengo wakasiya, ndinasemanso magome awiri amiyala onga oyamba aja, ndi kukwera m'phirimo, magome awiri ali m'manja mwanga.
4Ndipo analembera pamagome, monga mwa malembedwe oyamba, mau khumiwo, amene Yehova adanena ndi inu m'phirimo, ali pakati pa moto, tsiku la kusonkhanako; ndipo Yehova anandipatsa awa.
5Ndipo ndinatembenuka ndi kutsika m'phiri, ndi kuika magome m'likasa ndinalipanga, ali m'menemo monga Yehova anandilamulira ine.
6Ndipo ana a Israele anayenda ulendo wao kuchokera ku zitsime za ana a Yaakani kufikira ku Mosera. Kumeneko anamwalira Aroni, ndi kumeneko anamuika; ndipo Eleazara mwana wake anachita ntchito ya nsembe m'malo mwake.
7Kuchokerako ananka ulendo ku Gudigoda, ndi kuchokera ku Gudigoda kunka ku Yotibata, dziko la mitsinje yamadzi.
8Masiku aja Yehova anapatula fuko la Levi, linyamule likasa la chipangano la Yehova, liimirire pamaso pa Yehova kumtumikira, ndi kudalitsa m'dzina lake kufikira lero lino.
9Num. 18.20; Ezk. 44.28Chifukwa chake Levi alibe gawo kapena cholowa pamodzi ndi abale ake; Yehova mwini wake ndiye cholowa chake, monga Yehova Mulungu wake ananena naye.
10Ndipo ndinakhala m'phiri monga poyamba paja, masiku makumi anai usana ndi usiku; ndipo Yehova anandimvera ine pameneponso; Yehova sanafune kukuonongani.
11Ndipo Yehova anati kwa ine, Uka, tenga ulendo pamaso pa anthu; kuti alowe ndi kulandira dzikoli ndinalumbirira makolo ao kuti ndidzawapatsa.
Abwereza kuwadandaulira akonde namvere Mulungu12 Mik. 6.8 Ndipo tsopano, Israele, Yehova Mulungu wanu afunanji nanu, koma kuti muziopa Yehova Mulungu wanu, kuyenda m'njira zake zonse, ndi kukonda, ndi kutumikira Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse,
13kusunga malamulo a Yehova, ndi malemba ake, amene ndikuuzani lero kuti kukukomereni inu?
141Maf. 8.27Taonani thambo, ndi kumwambamwamba, dziko lapansi, ndi zonse zili m'mwemo ndi zake za Yehova Mulungu wanu.
15Deut. 4.37Koma Yehova anakondwera nao makolo anu kuwakonda, nasankha mbeu zao zakuwatsata, ndiwo inu, mwa mitundu yonse ya anthu, monga kuli lero lino.
16Yer. 4.4; Aro. 2.28-29Potero dulani khungu la mitima yanu, ndipo musamapulukiranso.
17Dan. 2.47; Aro. 2.11; Akol. 3.25Popeza Yehova Mulungu wanu ndiye Mulungu wa milungu, ndi Mbuye wa ambuye; Mulungu wamkulu, wamphamvu, ndi woopsa, wosasamalira nkhope za anthu, kapena kulandira chokometsera mlandu.
18Mas. 68.5Aweruzira ana amasiye ndi mkazi wamasiye; ndipo akonda mlendo, ndi kumpatsa chakudya ndi chovala.
19Eks. 22.21M'mwemo mukondane naye mlendo; popeza munali alendo m'dziko la Ejipito.
20Deut. 6.13Muziopa Yehova Mulungu wanu; mumtumikire Iyeyo; mummamatire Iye, ndi kulumbira pa dzina lake.
21Mas. 22.3Iye ndiye lemekezo lanu, Iye ndiye Mulungu wanu, amene anachita nanu zazikulu ndi zoopsa izi, mudaziona m'maso mwanu.
22Makolo anu anatsikira ku Ejipito ndiwo anthu makumi asanu ndi awiri; ndipo Yehova Mulungu wanu anakusandulizani tsopano muchuluke ngati nyenyezi za kumwamba.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.