MIYAMBO 21 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

1Mtima wa mfumu uli m'dzanja la Yehova ngati mitsinje ya madzi;

aulozetsa komwe afuna.

2 Luk. 16.15 Njira zonse za munthu zilungama pamaso pake;

koma Yehova ayesa mitima.

3 1Sam. 15.22; Yes. 1.11-15 Kuchita chilungamo ndi chiweruzo

kupambana ndi nsembe kumkonda Yehova.

4Maso akunyada, ndi mtima wodzikuza,

ndi nyali ya oipa, zili tchimo.

5Zoganizira za wakhama zichulukitsadi katundu;

koma yense wansontho angopeza umphawi.

6 2Pet. 2.3 Kupata chuma ndi lilime lonama

ndiko nkhungu yoyendayenda, ngakhale misampha ya imfa.

7Chiwawa cha amphulupulu chidzawakokolola;

chifukwa akana kuchita chiweruzo.

8Wosenza tchimo njira yake ikhotakhota;

koma ntchito ya woyera mtima ilungama.

9Kukhala pangodya ya tsindwi kufunika

kuposa kukhala m'nyumba ndi mkazi wolongolola.

10 Yak. 4.5 Wamphulupulu mtima wake umkhumba zoipa;

sakomera mtima mnzake.

11Polangidwa wonyoza, wachibwana alandira nzeru,

naphunzira pakuyang'ana pa wanzeru.

12Wolungama aganizira za nyumba ya wamphulupulu,

kuti amphulupulu amagwetsedwa, naona zoipa.

13 Mat. 18.30-33; Yak. 2.13 Wotseka makutu ake polira waumphawi,

nayenso adzalira koma osamvedwa.

14Mphatso ya m'tseri ipembedza mkwiyo,

ndi mtulo wa pamfunga ukali wolimba.

15Kuchita chiweruzo kukondweretsa wolungama;

koma kuwaononga akuchita mphulupulu.

16Munthu wosochera panjira ya nzeru

adzakhala m'msonkhano wa akufa.

17Wokonda zoseketsa adzasauka;

wokonda vinyo ndi mafuta sadzalemera.

18 Yes. 43.3-4 Wochimwa ndiye chiombolo cha wolungama;

ndipo wachiwembu adzalowa m'malo mwa oongoka mtima.

19 Miy. 21.9 Kukhala m'chipululu kufunika

kuposa kukhala ndi mkazi wolongolola ndi wong'ung'udza.

20 Mat. 25.3-4 Mokhala wanzeru muli katundu wofunika ndi mafuta;

koma wopusa angozimeza.

21 Mat. 5.6 Wolondola chilungamo ndi chifundo

apeza moyo, ndi chilungamo, ndi ulemu.

22Wanzeru akwera pa mzinda wa olimba,

nagwetsa mphamvu yake imene anaikhulupirira.

23 Yak. 3.2 Wosunga m'kamwa mwake ndi lilime lake

asunga moyo wake kumavuto.

24Wonyada wodzikuza dzina lake ndiye wonyoza;

achita mwaukali modzitama.

25Chifuniro cha waulesi chimupha;

chifukwa manja ake akana kugwira ntchito.

26 Mas. 112.6, 9 Ena asirira modukidwa tsiku lonse;

koma wolungama amapatsa osamana.

27 Gen. 4.5; Yer. 6.19-20; Amo. 5.21-22 Nsembe ya oipa inyansa;

makamaka pakudza nayo iwo mwachiwembu.

28Mboni yonama idzafa;

koma mwamuna wakumvetsa adzanena mosakayika.

29Munthu woipa aumitsa nkhope yake;

koma woongoka mtima akonza njira zake.

30 Yer. 9.23-24; Mac. 5.39 Kulibe nzeru ngakhale luntha

ngakhale uphungu wotsutsana ndi Yehova.

31 Mas. 20.7; Yes. 31.1 Kavalo amakonzedweratu chifukwa cha tsiku la nkhondo;

koma wopulumutsa ndiye Yehova.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help