1Imvani Mulungu, mau anga, m'kudandaula kwanga;
sungani moyo wanga angandiopse mdani.
2Ndibiseni pa upo wachinsinsi wa ochita zoipa;
pa phokoso la ochita zopanda pake.
3Amene anola lilime lao ngati lupanga,
napiringidza mivi yao, ndiyo mau akuwawitsa;
4kuponyera wangwiro mobisika:
Amponyera modzidzimutsa, osaopa.
5 Miy. 1.11 Alimbikitsana m'chinthu choipa;
apangana za kutchera misampha mobisika;
akuti, Adzaiona ndani?
6Afunafuna zosalungama; kusanthula, asanthuladi mpaka kutha;
chingakhale cha m'kati mwake mwa munthu, ndi mtima wozama.
7Koma Mulungu adzawaponyera muvi;
adzalaswa modzidzimutsa.
8 Miy. 18.7 Adzawakhumudwitsa, lilime lao lidzawatsutsa;
onse akuwaona adzawathawa.
9 Yer. 51.10 Ndipo anthu onse adzachita mantha;
nadzabukitsa chochita Mulungu,
nadzasamalira ntchito yake.
10 Mas. 32.11 Wolungama adzakondwera mwa Yehova,
nadzakhulupirira Iye;
ndipo oongoka mtima onse adzalemekeza.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.