MIYAMBO 6 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

Za kuperekera mnzake chikoleZisanu ndi ziwiri zoipira Mulungu

1 Miy. 11.15 Mwananga, ngati waperekera mnzako chikole,

ngati wapangana kulipirira mlendo,

2wakodwa ndi mau a m'kamwa mwako,

wagwidwa ndi mau a m'kamwa mwako.

3Chita ichi tsono; mwananga, nudzipulumutse;

popeza walowa m'dzanja la mnzako,

pita nudzichepetse, numdandaulire mnzako.

4Usaone tulo m'maso mwako,

ngakhale kuodzera zikope zako.

5Dzipulumutse wekha ngati mphoyo kudzanja la msaki,

ndi mbalame kudzanja la msodzi.

6 Yob. 12.7 Pita kunyerere, waulesi iwe,

penya njira zao nuchenjere;

7zilibe mfumu,

ngakhale kapitao, ngakhale mkulu;

8koma zitengeratu zakudya zao m'malimwe;

ndipo zituta dzinthu zao m'masika.

9Udzagona mpaka liti, waulesi iwe?

Udzauka kutulo tako liti?

10Tulo tapang'ono, kuodzera pang'ono,

kungomanga manja pang'ono, ndi kugona;

11ndipo umphawi wako udzafika ngati mbala,

ndi kusauka kwako ngati munthu wachikopa.

12Munthu wopanda pake, mwamuna wamphulupulu;

amayenda ndi m'kamwa mokhota.

13 Mas. 35.19 Amatsinzinira ndi maso ake, napalasira ndi mapazi ake,

amalankhula ndi zala zake;

14zopotoka zili m'mtima mwake, amaganizira zoipa osaleka;

amapikisanitsa anthu.

15 Yer. 19.11 Chifukwa chake tsoka lake lidzadza modzidzimuka;

adzasweka msangamsanga, palibe chompulumutsa.

16Zilipo zinthu zisanu ndi chimodzi Yehova azida;

ngakhale zisanu ndi ziwiri zimnyansa:

17 Mas. 101.5; 120.2; Yes. 1.15 Maso akunyada, lilime lonama,

ndi manja akupha anthu osachimwa;

18 Gen. 6.5; Yes. 59.7 mtima woganizira ziwembu zoipa,

mapazi akuthamangira mphulupulu m'mangum'mangu;

19 Eks. 20.16 mboni yonama yonong'ona mabodza,

ndi wopikisanitsa abale.

20 Aef. 6.1 Mwananga, sunga malangizo a atate wako,

usasiye malamulo a mai ako;

21uwamange pamtima pako osaleka;

uwalunze pakhosi pako.

22Adzakutsogolera ulikuyenda,

ndi kukudikira uli m'tulo,

ndi kulankhula nawe utauka.

23 Mas. 119.105 Pakuti malangizo ndi nyali, malamulo ndi kuunika;

ndi zidzudzulo za mwambo ndizo njira ya moyo.

24 Miy. 2.16 Zikutchinjiriza kwa mkazi woipa,

ndi kulilime losyasyalika la mkazi wachiwerewere.

25 Mat. 5.28 Asakuchititse kaso m'mtima mwako,

asakukole ndi zikope zake.

26 Ezk. 13.18 Pakuti ukayamba ndi mkazi wadama,

udzamaliza ndi nyenyeswa;

ndipo mkazi wa mwini amasaka moyo wa mtengowapatali.

27Kodi mwamuna angatenge moto pa chifuwa chake,

osatentha zovala zake?

28Pena kodi mwamuna angayende pa makala oyaka,

osapsa mapazi ake?

29Chomwecho wolowa kwa mkazi wa mnzake;

womkhudzayo sadzapulumuka chilango.

30Anthu sanyoza mbala ikaba,

kuti ikhutitse mtima wake pomva njala;

31koma ikapezedwa idzabwezera kasanu ndi kawiri;

idzapereka chuma chonse cha m'nyumba yake.

32Wochita chigololo ndi mkazi alibe nzeru;

wofuna kuononga moyo wakewake ndiye amatero.

33Adzalasidwa nanyozedwa;

chitonzo chake sichidzafafanizidwe.

34Pakuti nsanje ndiyo ukali wa mwamuna,

ndipo sadzachitira chifundo tsiku lobwezera chilango.

35Sadzalabadira chiombolo chilichonse,

sadzapembedzeka ngakhale uchulukitsa malipo.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help