DEUTERONOMO 15 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

Za chaka cha chilekerero(Lev. 25.1-7)

1Pakutha pake pa zaka zisanu ndi ziwiri pakhale chilekerero.

2Chilekererocho ndichi: okongoletsa onse alekerere chokongoletsa mnansi wake; asachifunse kwa mnansi wake, kapena mbale wake; popeza analalikira chilekerero cha Yehova.

3Muyenera kuchifunsa kwa mlendo; koma chanu chilichonse chili ndi mbale wanu, dzanja lanu lichilekerere;

4ndiko kuti pasakhale waumphawi mwa inu; pakuti Yehova adzakudalitsani kwambiri m'dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani likhale cholowa chanuchanu;

5chokhachi mumvere chimverere mau a Yehova Mulungu wanu, kuti musamalire kuchita malamulo awa onse amene ndikuuzani lero lino.

6Popeza Yehova Mulungu wanu adzakudalitsani, monga ananena nanu; ndipo mudzakongoletsa amitundu ambiri, osakongola nokha; nimudzachita ufumu pa amitundu ambiri, koma iwo sadzachita ufumu pa inu.

Za aumphawi ndi akapolo

7 1Yoh. 3.17 Akakhala ndi inu munthu waumphawi, ndiye wina wa abale anu, mu umodzi wa midzi yanu, m'dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani, musakhakala mtima wanu, kapena kuumitsa dzanja lanu kukaniza mbale wanu waumphawi;

8Mat. 5.42koma muzimtansira dzanja lanu ndithu ndi kumkongoletsa ndithu zofikira kusowa kwake, monga umo amasowa.

9Mat. 25.41-42Dzichenjerani, mungakhale mau opanda pake mumtima mwanu, ndi kuti, Chayandika chaka chachisanu ndi chiwiri, chaka cha chilekerero; ndipo diso lanu lingaipire mbale wanu waumphawi, osampatsa kanthu; ndipo iye angalirire inu kwa Yehova; ndipo mwa inu mungakhale tchimo.

102Ako. 9.5, 7Muzimpatsa ndithu, osawawa mtima wanu pompatsa; popeza, chifukwa cha ichi Yehova Mulungu wanu adzakudalitsani mu ntchito zanu zonse, ndi m'zonse muikapo dzanja lanu.

11Mat. 26.11Popeza waumphawi salekana m'dziko, chifukwa chake ndikuuzani ndi kuti, Dzanja lanu mulitansire ndithu mbale wanu, ndi ozunzika anu, ndi aumphawi anu, a m'dziko mwanu.

Lamulo la pa kapolo(Eks. 21.1-7)

12 Lev. 25.39; Yer. 34.14 Mukagula mbale wanu, Muhebri wamwamuna kapena Muhebri wamkazi, ndipo adzakutumikira zaka zisanu ndi chimodzi; koma chaka chachisanu ndi chiwiri umlole achoke kwanu waufulu.

13Ndipo pomlola iwe achoke kwanu waufulu, musamamlola achoke wopanda kanthu;

14mumlemeze nazo za nkhosa ndi mbuzi zanu, ndi za popondera mphesa, ndi za mosungira vinyo; monga Yehova Mulungu wanu anakudalitsani mumninkhe uyu.

15Ndipo mukumbukire kuti munali akapolo m'dziko la Ejipito, ndipo Yehova Mulungu wanu anakuombolani; chifukwa chake ndikuuzani ichi lero lino.

16Ndipo kudzakhala, akanena ndi inu, Sindituluka kuchoka kwanu; popeza akonda inu ndi nyumba yanu, popeza kumkomera kwanu;

17pamenepo muzitenga lisungulo, ndi kulipisa m'khutu mwake, kulikanikiza ndi chitseko, ndipo adzakhala kapolo wanu kosalekeza. Muzichitanso momwemo ndi adzakazi anu.

18Musamayesa nchosautsa, pomlola akuchokereni waufulu; popeza anakugwirirani ntchito zaka zisanu ndi chimodzi monga wolipidwa wakulandira chowirikiza; potero Yehova Mulungu wanu adzakudalitsani m'zonse muzichita.

Za nyama zoyamba kubadwa

19 Eks. 13.2 Zazimuna zonse zoyamba kubadwa, zobadwa mwa ng'ombe zanu ndi mwa nkhosa ndi mbuzi zanu, muzizipatulira Yehova Mulungu wanu; musamagwiritsa ntchito yoyamba kubadwa mwa ng'ombe zanu, kapena kusenga yoyamba kubadwa ya nkhosa kapena mbuzi zanu.

20Muzidye chaka ndi chaka pamaso pa Yehova Mulungu wanu, m'malo amene Yehova adzasankha, inu ndi a m'banja mwanu.

21Lev. 22.20; Aheb. 9.14Koma ikakhala nacho chilema, yotsimphina, kapena yakhungu, chilema chilichonse choipa, musamaiphera nsembe Yehova Mulungu wanu.

22Muidye m'mudzi mwanu; odetsa ndi oyera aidye chimodzimodzi, monga mphoyo ndi nswala.

23Mwazi wake wokha musamadya; muuthire pansi ngati madzi.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help