1Ndipo gawo la fuko la ana a Yuda monga mwa mabanja ao linafikira malire a Edomu, ku chipululu cha Zini kumwera, ku malekezero a kumwera.
2Ndi malire ao a kumwera, anayambira ku malekezero a Nyanja ya Mchere, ku nyondo yoloza kumwera;
3natuluka kumwera kwa chikweza cha Akarabimu, napitirira ku Zini, nakwera kumwera kwa Kadesi-Baranea, napitirira ku Hezironi, nakwera ku Adara, nazungulira ku Karika;
4napitirira ku Azimoni, natuluka ku mtsinje wa Ejipito; ndi malekezero a malirewa anali ku Nyanja Yaikulu; awa ndi malire anu a kumwera.
5Ndi malire a kum'mawa ndiwo Nyanja ya Mchere, mpaka mathiriro ake a Yordani. Ndi malire a kumpoto anayambira nyondo ya nyanja ku mathiriro a Yordani;
6nakwera malire kunka ku Betehogila, napitirira kumpoto kwa Betaraba; nakwera malire kunka ku mwala wa Bohani mwana wa Rubeni;
7nakwera malire kunka ku Debiri, kuchokera ku chigwa cha Akori, ndi kumpoto kupenyera Giligala ndiko kundunji kwa chikweza cha Adumimu, ndiko kumwera kwa mtsinje; napitirira malire kunka ku madzi a Enisemesi, ndi matulukiro ake anali ku Enirogele;
8nakwera malire kunka ku chigwa cha mwana wa Hinomu, kumbali kwa Ayebusi, kumwera, ndiko Yerusalemu; nakwera malire kunka kumwamba kwa phiri lokhala patsogolo pa chigwa cha Hinomu kumadzulo, ndilo ku mathero ake a chigwa cha Refaimu kumpoto.
9Ndipo analemba malire kuyambira pamwamba paphiri mpaka chitsime cha madzi cha Nefitowa, natulukira malire kumizinda ya phiri la Efuroni; ndipo analemba malire kunka ku Baala, ndiwo Kiriyati-Yearimu.
10Ndipo malire anazungulira kuyambira ku Baala kunka kumadzulo, kuphiri la Seiri, napitirira kumbali kwa phiri la Yearimu kumpoto, ndilo Kesaloni, natsikira ku Betesemesi, napitirira ku Timna;
11natuluka malire kunka ku mbali ya Ekeroni kumpoto; ndipo analemba malire kunka ku Sikeroni, napitirira kuphiri la Baala, natuluka ku Yabinele; ndipo matulukiro a malire anali kunyanja.
12Ndi malire a kumadzulo anali ku Nyanja Yaikulu ndiwo malire ake. Awa ndi malire a ana a Yuda pozungulira monga mwa mabanja ao.
13Koma Yoswa anampatsa Kalebe mwana wa Yefune gawo mwa ana a Yuda, monga Yehova adamlamulira, ndiwo mudzi wa Araba, ndiye atate wa Anaki, ndiwo Hebroni.
14Ndipo Kalebe anaingitsako ana aamuna atatu a Anaki, ndiwo Sesai, ndi Ahimani, ndi Talimai, ana a Anaki.
15Nakwera komweko kunka kwa nzika za Debiri; koma kale dzina la Debiri ndilo Kiriyati-Sefere.
16Ndipo Kalebe anati, Iye amene akantha Kiriyati-Sefere, naulanda, yemweyo ndidzampatsa Akisa mwana wanga akhale mkazi wake.
17Ower. 1.13Ndipo Otiniyele mwana wa Kenazi, mbale wake wa Kalebe, anaulanda; ndipo anampatsa Akisa mwana wake akhale mkazi wake.
18Ndipo kunali, m'mene anamdzera, anamkangamiza mwamuna wake kuti apemphe atate wake ampatse munda; ndipo anatsika pabulu; pamenepo Kalebe ananena naye, Ufunanji?
19Nati iye, Mundipatse dalitso; popeza mwandipatsa dziko la kumwera, ndipatseninso zitsime za madzi. Pamenepo anampatsa zitsime za kumtunda, ndi zitsime za kunsi.
20Ichi ndi cholowa cha fuko la ana a Yuda monga mwa mabanja ao.
21Ndipo mizinda ya ku malekezero a fuko la ana a Yuda ku malire a Edomu, kumwera ndiwo, Kabizeeli ndi Edere, ndi Yaguru;
22ndi Kina ndi Dimona, ndi Adada;
23ndi Kedesi, ndi Hazori, ndi Itinani;
24Zifi ndi Telemu ndi Bealoti;
25ndi Hazori-Hadata, ndi Keriyoti-Hezironi, ndiwo Hazori;
26Amama ndi Sema ndi Molada;
27ndi Hazara-Gada, ndi Hesimoni, ndi Betepeleti;
28ndi Hazara-Suwala, ndi Beereseba, ndi Biziyotiya;
29Baala, ndi Iyimu, ndi Ezemu;
30ndi Elitoladi, ndi Kesili ndi Horoma;
311Sam. 27.6ndi Zikilagi, ndi Madimana ndi Sanisana;
32ndi Lebaoti, ndi Silihimu, ndi Aini ndi Rimoni; mizinda yonse ndiyo makumi awiri kudza isanu ndi inai; pamodzi ndi midzi yao.
33 Gen. 48.19 Ku chigwa, Esitaoli, ndi Zora ndi Asina;
34ndi Zanowa, ndi Enganimu, Tapuwa, ndi Enamu;
35Yaramuti, ndi Adulamu, Soko, ndi Azeka;
36ndi Saaraimu, ndi Aditaimu, ndi Gedera, ndi Gederotaimu; mizinda khumi ndi inai pamodzi ndi midzi yao.
37Zenani, ndi Hadasa, ndi Megidali-Gadi;
382Maf. 14.7ndi Dileani, ndi Mizipa, ndi Yokotele;
39Lakisi ndi Bozikati ndi Egiloni;
40ndi Kaboni, ndi Lahamasi, ndi Kitilisi;
41ndi Gederoti, Betedagoni, ndi Naama, ndi Makeda; mizinda khumi ndi isanu ndi umodzi pamodzi ndi midzi yao.
42Libina ndi Eteri ndi Asani;
43ndi Ifuta ndi Asina ndi Nezibu;
44ndi Keila ndi Akizibu, ndi Maresa; mizinda isanu ndi inai pamodzi ndi midzi yao.
45Ekeroni pamodzi ndi mizinda yake ndi midzi yao;
46kuyambira ku Ekeroni mpaka kunyanja, yonse ya ku mbali ya Asidodi, pamodzi ndi midzi yao.
47Asidodi, mizinda yake ndi midzi yake; Gaza, mizinda yake ndi midzi yake; mpaka mtsinje wa Ejipito, ndi Nyanja Yaikulu ndi malire ake.
48Ndi kumapiri Samiri, ndi Yatiri, ndi Soko;
49ndi Dana, ndi Kiriyati-Sana, ndiwo Debiri;
50ndi Anabu, ndi Esitemowa, ndi Animu;
51ndi Goseni, ndi Holoni, ndi Gilo; mizinda khumi ndi umodzi pamodzi ndi midzi yao.
52Arabu, ndi Duma, ndi Esani;
53ndi Yanimu, ndi Betetapuwa, ndi Afeka;
54ndi Humata, ndi Kiriyati-Ariba, ndiwo Hebroni, ndi Ziyori; mizinda isanu ndi inai pamodzi ndi midzi yao.
55Maoni, Karimele, ndi Zifi, ndi Yuta;
56ndi Yezireele, ndi Yokodeamu, ndi Zanowa;
57Kaini, Gibea ndi Timna; mizinda khumi pamodzi ndi midzi yao.
58Halahulu, Betezuri, ndi Gedori,
59ndi Maarati, ndi Betanoti, ndi Elitekoni; mizinda isanu ndi umodzi pamodzi ndi midzi yao.
60Kiriyati-Baala, ndiwo Kiriyati-Yearimu ndi Raba; mizinda iwiri pamodzi ndi midzi yao.
61M'chipululu, Betaraba, Midini, ndi Sekaka;
62ndi Nibisani, ndi Mzinda wa Mchere, ndi Engedi; mizinda isanu ndi umodzi pamodzi ndi midzi yao.
63 Ower. 1.21; 2Sam. 5.6 Koma ana a Yuda sanakhoze kuingitsa Ayebusi, nzika za Yerusalemu: m'mwemo Ayebusi anakhala pamodzi ndi ana a Yuda, ku Yerusalemu, mpaka lero lino.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.