MIYAMBO 30 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

Chivomerezo, pemphero ndi malangizo a Aguri

1Mau a Aguri mwana wa Yake; uthenga.

Munthuyo anati, Ndadzitopetsa, Mulungu;

ndadzitopetsa, Mulungu, ndathedwa;

2pakuti ndipambana anthu onse kupulukira,

ndilibe luntha la munthu.

3Sindinaphunzire nzeru

ngakhale kudziwa Woyerayo.

4 Yoh. 3.13 Ndani anakwera kumwamba natsikanso?

Ndani wakundika nafumbata mphepo?

Ndani wamanga madzi m'malaya ake?

Ndani wakhazikitsa matsiriziro onse a dziko?

Dzina lake ndani? Dzina la mwanake ndani? Kapena udziwa.

5 Mas. 12.6; 18.30 Mau onse a Mulungu ali oyengeka;

ndiye chikopa cha iwo amene amkhulupirira.

6 Deut. 4.2; Chiv. 22.18-19 Usaonjezere kanthu pa mau ake,

angakudzudzule, nungatsutsidwe kuti ulikunama.

7Zinthu ziwiri ndakupemphani,

musandimane izo ndisanamwalire:

8 Mat. 6.11 Mundichotsere kutali zachabe ndi mabodza;

musandipatse umphawi, ngakhale chuma,

mundidyetse zakudya zondiyenera;

9 Deut. 8.12, 14, 17; Neh. 9.25-26 ndingakhute ndi kukukanani, ndi kuti, Yehova ndani?

Kapena ndingasauke ndi kuba,

ndi kutchula dzina la Mulungu wanga pachabe.

10Usanamizire kapolo kwa mbuyake,

kuti angakutemberere nawe ndi kutsutsidwa.

11Pali mbadwo wotemberera atate ao,

osadalitsa amai ao.

12 Luk. 18.11 Pali mbadwo wodziyesa oyera,

koma osasamba litsiro lao.

13Pali mbadwo wokwezatu maso ao,

zikope zao ndi kutukula.

14 Mas. 52 Pali mbadwo mano ao akunga malupanga,

zibwano zao zikunga mipeni;

kuti adye osauka kuwachotsa kudziko,

ndi aumphawi kuwachotsa mwa anthu.

15Msundu uli ndi ana aakazi awiri ati, Patsa, patsa.

Pali zinthu zitatu sizikhuta konse,

ngakhale zinai sizinena, Kwatha:

16 Hab. 2.5 Manda, ndi chumba,

dziko losakhuta madzi,

ndi moto wosanena, Kwatha.

17 Gen. 9.29; Lev. 20.2 Diso lochitira atate wake chiphwete,

ndi kunyoza kumvera amake,

makwangwala a kumtsinje adzalikolowola,

ana a mphungu adzalidya.

18Zinthu zitatu zindithetsa nzeru,

ngakhale zinai, sindizidziwa:

19Njira ya mphungu m'mlengalenga,

njira ya njoka pamwala,

njira ya ngalawa pakati pa nyanja,

njira ya mwamuna ndi namwali.

20Chomwecho njira ya mkazi wachigololo;

adya, napukuta pakamwa, nati,

Sindinachite zoipa.

21Chifukwa cha zinthu zitatu dziko linthunthumira;

ngakhale chifukwa cha zinai silingathe kupirira nazo;

22chifukwa cha kapolo pamene ali mfumu;

ndi chitsiru chitakhuta zakudya;

23chifukwa cha mkazi wodedwa wokwatidwa;

ndi mdzakazi amene adzalandira cholowa cha mbuyake.

24Zilipo zinai zili zazing'ono padziko;

koma zipambana kukhala zanzeru:

25 Miy. 6.6-8 Nyerere ndi mtundu wosalimba,

koma zitengeratu zakudya zao m'malimwe.

26Mbira ndi mtundu wopanda mphamvu,

koma ziika nyumba zao m'matanthwe.

27Dzombe lilibe mfumu,

koma lituluka lonse mabwalomabwalo.

28Buluzi ungamgwire m'manja,

koma ali m'nyumba za mafumu.

29Pali zinthu zitatu ziyenda chinyachinya;

ngakhale zinai ziyenda mwaufulu:

30Mkango umene uposa zilombo kulimba,

supatukira chinthu chilichonse;

31tambala wolimba m'chuuno, ndi tonde,

ndi mfumu yokhala ndi ankhondo ake.

32 Mik. 7.16 Ngati wapusa podzikweza,

ngakhale kuganizira zoipa, tagwira pakamwa.

33Pakuti potakasa mkaka, mafuta ayengekapo;

ndi popsinja mfuno, mwazi utulukamo,

ndi polimbikira mkwiyo ndeu ionekamo.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help