AHEBRI Mau Oyamba - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu
Mau OyambaMlembi wa Kalata yolembera kwa Ahebri akufuna kuwalimbitsa mtima Akhristu ena okhala pakati pa anthu ena amene amawavutitsa, kuti asafooke pa chikhulupiriro chao, kuwopa kuti angasiye Chikhristu. Awaonetsa kuti chikhulupiriro choona maziko ake ndi Yesu Khristu, Mwana wa Mulungu, Wansembe wamuyaya, amene apulumutsa omkhulupirira pakuwayanjanitsa ndi Mulungu.Iye yekha pokhala Mkulu wa ansembe atha kupulumutsa anthu okhulupirira kumachimo, mantha ndi imfa; nsembe zakale zija zinkangofanizira nsembe yeniyeni yomwe Yesu adaipereka pakufera anthu onse.Mau aakulu mu buku limeneli ali pa 5.8-9 pamene akunena za Yesu kuti, “angakhale anali Mwana, anaphunzira kumvera ndi izi adamva kuwawa nazo; ndipo pamene anakonzeka wamphumphu anakhala kwa onse akumvera Iye chifukwa cha chipulumutso chosatha.”Pa mutu 11 iye akupereka zitsanzo za chikhulupiriro cha Aisraele ena otchuka, ndipo akuwauza awerengi ake kuti akhalebe okhulupirika. Pa mutu 12, akuwauzanso kuti akhalebe wokhulupirika mpaka mapeto, nakhazike maso ao pa Yesu, ndi kupirira pamene akumana ndi mazunzo kapena masautso. Bukuli likumaliza ndi malangizo komanso machenjezo.Za mkatimuMulungu adziwululira chonse kudzera mwa Khristu 1.1-3Za ukulu wake wa Khristu, Mwana wa Mulungu 1.4—4.13Aposa angelo 1.4-14Khristu mtsogoleri wa chipulumutso 2.1-18Aposa Mose yemwe 3.1—4.13Za ukulu wa unsembe wa Khristu 4.14—10.39Unsembe wake ndi wamuyaya, apambana Melkizedeki 4.14—7.28Ukulu wa chipangano chake 8.1—9.28Ukulu wa nsembe yake 10.1-38Za chikhulupiriro cha anthu ake 11.1-40Za chitsanzo cha Yesu Khristu 12.1-29Mau otsiriza: za m'mene tingakondweretsere Mulungu 13.1-25