RUTE Mau Oyamba - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu
Mau OyambaBukuli likamba nkhani ya Rute, mkazi wachimowabu amene adakwatiwa ndi mwamuna wa ku Israele. Mwamuna wake atamwalira, iye atsatira mpongozi wake Naomi ku Betelehemu kwao chifukwa chokhulupirira Mulungu wa Aisraele.Nkhani yabwinoyi yochitika panthawi ija yankhanza ya Oweruza, iwonetsa kuti ngakhale amitundu nawonso adzalandira madalitso a Mulungu, akakhulupirira Mulungu wa Israele ndi kusanduka anthu ake.Za mkatimuNaomi abwerera ku Betelehemu pamodzi ndi Rute 1.1-22Rute akumana ndi Bowazi 2.1—3.18Rute akwatiwa ndi Bowazi Davide 4.1-22