1 MBIRI 13 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

Apita nalo likasa nalisunga m'nyumba ya Obededomu(2Sam. 6.1-11)

1Ndipo Davide anafunsana ndi akulu a zikwi ndi a mazana, inde atsogoleri ali onse.

2Ndipo Davide anati kwa msonkhano wonse wa Israele, Chikakomera inu, ndipo chikachokera kwa Yehova Mulungu wathu, titumize konse kuti abale athu otsala m'dziko lonse la Israele, ndi ansembe ndi Alevi okhala nao m'mizinda yao yokhala napo podyetsa, kuti asonkhane kwa ife;

3ndipo tibwere nalo kwa ife likasa la Mulungu wathu, pakuti sitinafunako masiku a Saulo.

4Ndipo a msonkhano onse anati kuti adzachita; pakuti chidayenera chinthuchi pamaso pa anthu onse.

5M'mwemo Davide anamemeza Aisraele onse kuyambira Sihori wa ku Ejipito mpaka polowera ku Hamati, kutenga likasa la Mulungu ku Kiriyati-Yearimu.

6Eks. 25.18, 22Ndipo Davide ndi Aisraele onse pamodzi naye anakwera kunka ku Baala, ndiko ku Kiriyati-Yearimu wa mu Yuda, kukwera nalo kuchokera komweko likasa la Mulungu Yehova wakukhala pa akerubi, kumene aitanirako Dzina.

71Sam. 7.1Ndipo anatengera likasa la Mulungu pa galeta watsopano kuchokera kunyumba ya Abinadabu; ndi Uza ndi Ahiyo anayendetsa ng'ombe za pa galetayo.

82Sam. 6.5Ndipo Davide ndi Aisraele onse anasewera pamaso pa Mulungu ndi mphamvu yao yonse; ndi nyimbo, ndi azeze, ndi zisakasa, ndi malingaka, ndi nsanje, ndi malipenga.

9Ndipo pamene anafika ku dwale la Kidoni, Uza anatambasula dzanja lake kulichirikiza likasa, pakuti ng'ombe zikadapulumuka.

10Num. 4.15Ndi mkwiyo wa Yehova unayakira Uza, namkantha, chifukwa anatambasulira likasa dzanja lake, nafa komweko pamaso pa Mulungu.

11Ndipo kudaipira Davide kuti Yehova adachita chipasulo ndi Uza; motero anatcha malowo Pereziuza, mpaka lero lino.

12Ndipo Davide anaopa Mulungu tsikulo, kuti, Ndidzafika nalo bwanji likasa la Mulungu kwathu?

13M'mwemo Davide sanafike nalo likasa kwao kumzinda wa Davide, koma analipambutsira kunyumba ya Obededomu wa ku Giti.

142Sam. 6.11Ndi likasa la Mulungu linakhala ndi banja la Obededomu m'nyumba mwake miyezi itatu; ndipo Yehova anadalitsa nyumba ya Obededomu, ndi zonse anali nazo.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help