1 Aef. 3.1; Akol. 1.10 Ndikudandaulirani inu tsono, ine wandende mwa Ambuye, muyende koyenera maitanidwe amene munaitanidwa nao,
2Mac. 20.19; Afi. 2.3ndi kuonetsera kudzichepetsa konse, ndi chifatso, ndi kuonetsera chipiriro, ndi kulolerana wina ndi mnzake, mwa chikondi;
3Akol. 3.14ndi kusamalitsa kusunga umodzi wa Mzimu mwa chimangiriro cha mtendere.
41Ako. 12.4, 11Thupi limodzi ndi Mzimu mmodzi, monganso anakuitanani m'chiyembekezo chimodzi cha maitanidwe anu;
51Ako. 1.13Ambuye mmodzi, chikhulupiriro chimodzi, ubatizo umodzi,
61Ako. 8.6Mulungu mmodzi ndi Atate wa onse amene ali pamwamba pa onse, ndi mwa onse, ndi m'kati mwa zonse.
7Aro. 12.3, 6Ndipo kwa yense wa ife chapatsika chisomo, monga mwa muyeso wa mphatso ya Khristu.
8 Mas. 68.18 Chifukwa chake anena,
M'mene anakwera kumwamba, anamanga ndende undende,
naninkha zaufulu kwa anthu.
9 Yoh. 6.33, 62 Koma ichi, chakuti, Anakwera, nchiyani nanga koma kuti anatsikiranso ku madera a kunsi kwa dziko?
10Mac. 1.9, 11Iye wotsikayo ndiye yemweyonso anakwera, popitiriratu miyamba yonse, kuti akadzaze zinthu zonse.
111Ako. 12.28Ndipo Iye anapatsa ena akhale atumwi; ndi ena aneneri; ndi ena alaliki; ndi ena abusa, ndi ena aphunzitsi;
121Ako. 12.7, 27kuti akonzere oyera mtima kuntchito ya utumiki, kumangirira thupi la Khristu;
13Akol. 1.28; 2.2-3kufikira ife tonse tikafikira ku umodzi wa chikhulupiriro, ndi wa chizindikiritso cha Mwana wa Mulungu, kwa munthu wangwiro, ku muyeso wa msinkhu wa chidzalo cha Khristu.
14Aheb. 13.9Kuti tisakhalenso makanda, ogwedezekagwedezeka, natengekatengeka ndi mphepo yonse ya chiphunzitso, ndi tsenga la anthu, ndi kuchenjerera kukatsata chinyengo cha kusocheretsa;
15Zek. 8.16; 2Ako. 4.2; Akol. 1.18koma ndi kuchita zoona mwa chikondi tikakule m'zinthu zonse, kufikira Iye amene ali mutu ndiye Khristu;
16Akol. 2.19kuchokera mwa Iye thupi lonse, lolukidwa ndi lolumikizidwa pamodzi, pothandizanapo mfundo yonse, monga mwa kuchititsa kwa chiwalo chonse pa muyeso wake, lichita makulidwe a thupi, kufikira chimango chake mwa chikondi.
Kusiyana kwa kuyera mtima kwa Chikhristu ndi mayendedwe oipa a akunja17 Aef. 2.1-2 Pamenepo ndinena ichi, ndipo ndichita umboni mwa Ambuye, kuti simuyendanso inu monganso amitundu angoyenda, m'chitsiru cha mtima wao,
18Aef. 2.12odetsedwa m'nzeru zao, oyesedwa alendo pa moyo wa Mulungu, chifukwa cha chipulukiro chili mwa iwo, chifukwa cha kuumitsa kwa mitima yao;
19Aro. 1.24, 26amenewo popeza sazindikiranso kanthu konse, anadzipereka okha kuti akhumbe zonyansa, kuti achite chidetso chonse mu umbombo.
20Koma inu simunaphunzire Khristu chotero,
21Aef. 1.13ngatitu mudamva Iye, ndipo munaphunzitsidwa mwa Iye, monga choonadi chili mwa Yesu;
22Aro. 6.6kuti muvule, kunena za makhalidwe anu oyamba, munthu wakale, wovunda potsata zilakolako za chinyengo;
23Akol. 3.10koma kuti mukonzeke, mukhale atsopano mu mzimu wa mtima wanu,
24Akol. 3.10nimuvale munthu watsopano, amene analengedwa monga mwa Mulungu, m'chilungamo, ndi m'chiyero cha choonadi.
25 Aro. 12.5; Aef. 4.15 Mwa ichi, mutataya zonama, lankhulani zoona yense ndi mnzake; pakuti tili ziwalo wina ndi mnzake.
26Mas. 37.8Kwiyani, koma musachimwe; dzuwa lisalowe muli chikwiyire,
27Yak. 4.7ndiponso musampatse malo mdierekezi.
281Ate. 4.11Wakubayo asabenso; koma makamaka agwiritse ntchito, nagwire ntchito yokoma ndi manja ake, kuti akhale nacho chakuchereza wosowa.
29Akol. 3.8, 16Nkhani yonse yovunda isatuluke m'kamwa mwanu, koma ngati pali ina yabwino kukumangirira monga mofunika ndiyo, kuti ipatse chisomo kwa iwo akumva.
30Yes. 63.10; Aef. 1.13Ndipo musamvetse chisoni Mzimu Woyera wa Mulungu, amene munasindikizidwa chizindikiro mwa Iye, kufikira tsiku la maomboledwe.
31Akol. 3.8, 19Chiwawo chonse, ndi kupsa mtima, ndi mkwiyo, ndi chiwawa, ndi mwano zichotsedwe kwa inu, ndiponso choipa chonse.
32Mrk. 11.25; 1Pet. 3.8-9Koma mukhalirane okoma wina ndi mnzake, a mtima wachifundo, akukhululukirana nokha, monganso Mulungu mwa Khristu anakhululukira inu.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.