YOWELE Mau Oyamba - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu
Mau OyambaYowele adalalikira makamaka pa nthawi ya ufumu wa Persiya, koma za moyo wake sitidziwa bwino. Iye akamba za mliri wa dzombe ndi chilala; zimene zaonongeratu mbeu zonse ndi mitengo yomwe. Mneneriyu aona ngati ichi ndi chizindikiro chosonyeza kuti tsiku la Yehova lidzabwera pamene Mulungu adzalanga anthu onse okana malamulo ake. Tsono Yowele akuwapempha anthuwo kuti atembenuke mtima ndi kubwerera kwa Chauta, poyembekeza kuti mwina Mulungu adzawakhulukira ndi kuwadalitsa monga adawalonjezera. Mau ena odziwika ndi akuti lidzafika tsiku pamene Yehova adzatuma mzimu wake pa anthu onse, aamuna ndi aakazi, achikulire ndi achinyamata omwe.Za mkatimuMliri wa dzombe 1.1—2.17 Lonjezo la kukonzedwanso kwa zinthu 2.18-27Tsiku la Ambuye 2.28—3.21