AHEBRI 2 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

Yesu Khristu Nkhoswe yathu yakuposa angelo akhoza kumva nafe chifundo

1Mwa ichi tiyenera kusamaliradi zimene tidazimvazi kuti kapena tingatengedwe ndi kusiyana nazo.

2Num. 15.30-31Pakuti ngati mau adalankhulidwa ndi angelo adakhala okhazikika, ndipo cholakwira chilichonse ndi chosamvera chalandira mphotho yobwezera yolungama,

3Aheb. 10.28-29; Mat. 4.17tidzapulumuka bwanji ife, tikapanda kusamala chipulumutso chachikulu chotero? Chimene Ambuye adayamba kuchilankhula, ndipo iwo adachimva anatilimbikitsira ife;

4Mac. 14.3; 1Ako. 12.4, 7, 11pochita umboni pamodzi nao Mulungunso ndi zizindikiro, ndi zozizwitsa ndi mphamvu za mitundumitundu ndi zogawira za Mzimu Woyera, monga mwa chifuniro chake.

5Pakuti sanagonjetsere angelo dziko lilinkudza limene tinenali.

6Mas. 45.6-7Koma wina anachita umboni pena, nati,

Munthu nchiyani kuti mumkumbukira iye?

Kapena mwana wa munthu kuti mucheza naye?

7 Mas. 8.4-6 Munamchepsa pang'ono ndi angelo,

mudamveka iye korona wa ulemerero ndi ulemu,

ndipo mudamuika iye woyang'anira ntchito za manja anu;

8 Mat. 28.18; 1Ako. 15.25 mudagonjetsa zonse pansi pa mapazi ake.

Pakuti muja adagonjetsa zonse kwa iye, sanasiyepo kanthu kosamgonjera iye. Koma sitinayambe tsopano apa kuona zonse zimgonjera.

9Afi. 2.7-9; Yoh. 3.16Koma timpenya Iye amene adamchepsa pang'ono ndi angelo, ndiye Yesu, chifukwa cha zowawa za imfa, wovala korona wa ulemerero ndi ulemu, kuti ndi chisomo cha Mulungu alawe imfa m'malo mwa munthu aliyense.

10Aro. 11.36; Aheb. 5.8-9Pakuti kunamuyenera Iye amene zonse zili chifukwa cha Iye, ndi zonse mwa Iye, pakutenga ana ambiri alowe ulemerero, kumkonza wamphumphu mtsogoleri woyamba wa chipulumutso chao mwa zowawa.

11Aheb. 10.10, 14Pakuti Iye wakuyeretsa ndi iwo akuyeretsedwa achokera onse mwa mmodzi; chifukwa cha ichi alibe manyazi kuwatcha iwo abale.

12Mas. 22.22; Mac. 27.25Ndi kuti,

Ndidzalalikira dzina lanu kwa abale anga,

pakati pa Mpingo ndidzakuimbirani.

13 Mas. 18.2; Yes. 8.18 Ndiponso,

Ndidzamtama Iye.

Ndiponso,

Taonani, Ine ndi ana amene Mulungu anandipatsa.

14 Yoh. 1.14; 1Ako. 15.54-55 Popeza tsono ana ndiwo a mwazi ndi nyama, Iyenso momwemo adalawa nao makhalidwe omwewo kuti mwa imfa akamuononge iye amene anali nayo mphamvu ya imfa, ndiye mdierekezi;

15Aro. 8.15nakamasule iwo onse amene, chifukwa cha kuopa imfa, m'moyo wao wonse adamangidwa ukapolo.

16Pakuti ndithu salandira angelo, koma alandira mbeu ya Abrahamu.

17Afi. 2.7; Aheb. 4.15-16Potero kudamuyenera kufanizidwa ndi abale m'zonse, kuti akadzakhala mkulu wa ansembe wachifundo ndi wokhulupirika m'zinthu za kwa Mulungu, kuti apereke dipo la zoipa za anthu.

18Aheb. 4.15-16Pakuti popeza adamva zowawa, poyesedwa yekha, akhoza kuthandiza iwo amene ayesedwa.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help