1 Deut. 31.17; Mas. 44.24 Mudzandiiwala chiiwalire, Yehova, kufikira liti?
Mudzandibisira ine nkhope yanu kufikira liti?
2Ndidzachita uphungu m'moyo mwanga kufikira liti,
pokhala ndi chisoni m'mtima mwanga tsiku lonse?
Adzandiukira ine mdani wanga kufikira liti?
3 Ezr. 9.8 Penyani, ndiyankheni, Yehova Mulungu wanga.
Penyetsani maso anga, kuti ndingagone tulo ta imfa;
4 Mas. 25.2 kuti anganene mdani wanga, Ndamgonjetsa;
ndipo angakondwere otsutsana nane posunthika ine.
5 Mas. 33.21 Koma ine ndakhulupirira pa chifundo chanu;
mtima wanga udzakondwera nacho chipulumutso chanu.
6 Mas. 116.7 Ndidzaimbira Yehova,
pakuti anandichitira zokoma.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.