1 Mas. 102.13; Yes. 60.4-5, 10; Zek. 1.17; Aef. 2.12-13 Pakuti Yehova adzamchitira chifundo Yakobo, ndipo adzasankhanso Israele, ndi kuwakhazikitsa m'dziko la kwao; ndipo achilendo adzadziphatika okha kwa iwo, nadzadzigumikiza kunyumba ya Yakobo.
2Ndipo mitundu ya anthu idzawatenga, ndi kuwafikitsa kumalo a kwao; ndipo a nyumba ya Israele adzakhala nao amitunduwo m'dziko la Yehova, ndi kuwayesa atumiki ndi adzakazi, ndipo amitunduwo adzatengedwa ndende, ndi amenewo anali ndende zao; ndipo Aisraele adzalamulira owavuta.
3Ndipo padzakhala tsiku loti Yehova adzakupumitsa chisoni chako, ndi nsautso yako, ndi ntchito yako yovuta, imene anakugwiritsa,
4Hab. 2.6pamenepo udzaimbira mfumu ya ku Babiloni nyimbo iyi yanchinchi, ndi kuti, Wovuta wathadi? Mudzi wagolide wathadi!
5Yehova wathyola mkunkhu wa woipa, ndodo yachifumu ya wolamulira.
6Wokantha anthu mwaukali kuwakantha chikanthire, wolamulira amitundu mokwiya, angosautsidwa wopanda womlanditsa.
7Dziko lonse lapuma, lili duu; iwo ayamba kuimba nyimbo.
8Inde, milombwa ikondwera ndi iwe, ndi mikungudza ya Lebanoni, ndi kunena, Chigwetsere iwe pansi, palibe wokwera kudzatidula ife.
9Kunsi kwa manda kugwedezeka, chifukwa cha iwe, kukuchingamira podza pako; kukuutsira iwe mizimu, ngakhale onse akuluakulu a dziko lapansi; kukweza kuchokera m'mipando yao mafumu onse a amitundu.
10Onse adzavomera, nadzati kwa iwe, Kodi iwe wakhalanso wopanda mphamvu ngati ife? Kodi iwe wafanana nafe?
11Chifumu chako chatsitsidwa kunsi kumanda, ndi phokoso la mingoli yako; mphutsi zayalidwa pansi pa iwe, ndi mphukutu zakukuta.
12Yes. 34.4Wagwadi kuchokera kumwamba, iwe nthanda, mwana wa mbandakucha! Wagwetsedwa pansi, iwe wolefula amitundu!
13Mat. 11.23Ndipo iwe unati mumtima mwako, Ndidzakwera kumwamba, ndidzakweza mpando wanga wachifumu pamwamba pa nyenyezi za Mulungu; ndidzakhala pamwamba paphiri la khamu, m'malekezero a kumpoto;
142Ate. 2.4ndidzakwera pamwamba pa mitambo, ndidzafanana ndi Wam'mwambamwamba.
15Koma udzatsitsidwa kunsi kumanda, ku malekezero a dzenje.
16Iwo amene akuona iwe adzayang'anitsitsa iwe, nadzalingalira za iwe, ndi kuti, Kodi uyu ndi munthu amene ananthunthumiritsa dziko lapansi, amene anagwedeza maufumu;
17amene anapululutsa dziko, napasula mizinda yake, amene sanamasule ndende zake, zinke kwao?
18Mafumu onse a amitundu, onsewo agona mu ulemerero yense kunyumba kwake.
19Koma iwe watayidwa kunja kwa manda ako, ngati nthambi yonyansa, ngati chovala cha ophedwa, opyozedwa ndi lupanga, otsikira kumiyala ya dzenje, monga ngati mtembo wopondedwa ndi phazi.
20Mas. 21.8, 10Iwe sudzaphatikizidwa pamodzi nao poikidwa, pakuti iwe waononga dziko lako, wapha anthu ako; mbeu ya ochita zoipa sidzatchulidwa konse.
21Eks. 20.5; Mat. 23.35Konzani inu popherapo ana ake, chifukwa cha kuipa kwa atate ao; kuti iwo asadzuka ndi kukhala nalo dziko, ndi kudzaza dziko lapansi ndi mizinda.
22Yob. 18.5, 19Ndipo Ine ndidzawaukira, ati Yehova wa makamu, ndi kuononga ku Babiloni dzina ndi otsala, ndi mwana wamwamuna, ndi chidzukulu chachimuna, ati Yehova.
23Zef. 2.13-14Ndidzayesapo pokhala nungu, ndi maiwe a madzi; ndipo ndidzasesapo ndi tsache la chionongeko, ati Yehova wa makamu.
Aneneratu za kuthyoka kwa Asiriya24Yehova wa makamu walumbira, nati, Ndithu monga ndaganiza, chotero chidzachitidwa; ndipo monga ndapanga uphungu, chotero chidzakhala;
25kuti Ine ndidzathyola Aasiriya m'dziko langa, ndi pamwamba pa mapiri anga ndidzawapondereza; pomwepo goli lake lidzachoka pa iwo, ndi katundu wake adzachoka paphewa pao.
26Umenewu ndi uphungu wopangira dziko lonse; ndipo ili ndi dzanja lotambasulidwa pa amitundu onse.
272Mbi. 20.6; Dan. 4.31, 35Pakuti Yehova wa makamu wapanga uphungu, ndani adzauleketsa? Ndi dzanja lake latambasulidwa, ndani adzalibweza?
Aneneratu za tsoka la Afilisti28 2Maf. 16.20 Chaka chimene mfumu Ahazi anamwalira katundu amene analipo.
29Usakondwere, iwe Filistiya, wonsewe, pothyoka ndodo inakumenya; pakuti m'muzu wa njoka mudzatuluka mphiri, ndimo chipatso chake chidzakhala njoka yamoto youluka.
30Ndi oyamba kubadwa a osauka adzadya, aumphawi nadzagona pansi osatekeseka; ndipo ndidzapha muzu wako ndi njala, ndi otsala ako adzaphedwa.
31Lira, chipata iwe; fuula, mzinda iwe; wasungunuka, Filistiya wonsewe, pakuti utsi uchokera kumpoto, ndipo palibe wosokera m'mizere yake.
32Mas. 87.1, 5; Zef. 3.12Ndipo adzayankhanji amithenga a amitundu? Kuti Yehova wakhazikitsa Ziyoni, ndipo m'menemo anthu ake ovutidwa adzaona pobisalira.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.