AROMA 15 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

Khristu chitsanzo cha kusamalirana kumene

1 Aro. 14.1; Agal. 6.1 Ndipo ife amene tili olimba tiyenera kunyamula zofooka za opanda mphamvu, ndi kusadzikondweretsa tokha.

21Ako. 10.33Yense wa ife akondweretse mnzake, kumchitira zabwino, zakumlimbikitsa.

3Afi. 2.5, 8; Mas. 69.9Pakuti Khristunso sanadzikondweretse yekha; koma monga kwalembedwa, Minyozo ya iwo amene anakunyoza iwe inagwa pa Ine.

4Aro. 4.23-24Pakuti zonse zinalembedwa kale zinalembedwa kutilangiza, kuti mwa chipiriro ndi chitonthozo cha malembo, tikhale ndi chiyembekezo.

5Aro. 12.16Ndipo Mulungu wa chipiriro ndi wa chitonthozo apatse inu kuti mukhale ndi mtima umodzi wina ndi mnzake, monga mwa Khristu Yesu;

6Mac. 4.24kuti nonse pamodzi, m'kamwa mmodzi, mukalemekeze Mulungu ndi Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu.

7Aro. 14.1, 3Chifukwa chake mulandirane wina ndi mnzake, monganso Khristu anakulandirani inu, kukachitira Mulungu ulemerero.

8Mat. 15.24Ndipo ndinena kuti Khristu anakhala mtumiki wa mdulidwe, chifukwa cha choonadi cha Mulungu, kuti alimbikitse malonjezo opatsidwa kwa makolo,

9Mas. 18.49; Yoh. 10.16ndi kuti anthu a mitundu ina akalemekeze Mulungu, chifukwa cha chifundo; monga kwalembedwa,

Chifukwa cha ichi ndidzakuvomerezani Inu

pakati pa anthu amitundu,

ndidzaimbira dzina lanu.

10 Deut. 32.43 Ndiponso anena, Kondwani, amitundu inu, pamodzi ndi anthu ake.

11 Mas. 117.1 Ndiponso,

Tamandani Ambuye, inu a mitundu yonse;

ndipo anthu onse amtamande.

12 Yes. 11.1, 10 Ndiponso, Yesaya ati,

Padzali muzu wa Yese,

ndi Iye amene aukira kuchita ufumu pa anthu amitundu;

Iyeyo anthu amitundu adzamuyembekezera.

13 Aro. 14.17 Ndipo Mulungu wa chiyembekezo adzaze inu ndi chimwemwe chonse ndi mtendere m'kukhulupirira, kuti mukachuluke ndi chiyembekezo, mu mphamvu ya Mzimu Woyera.

Utumwi wake ndi zotsimikiza mtima za Paulo

14 Aro. 11.13 Koma ine ndekhanso, abale anga, nditsimikiza mtima za inu, kuti inu nokhanso muli odzala ndi ubwino, odzazidwa ndi kudziwitsa konse, ndi kukhoza kudandaulirana wina ndi mnzake.

15Koma mwina ndaposa kukulemberani molimba mtima monga kukukumbutsaninso, chifukwa cha chisomo chapatsidwa kwa ine ndi Mulungu,

16Yes. 66.20; Aro. 11.13kuti ndikhale mtumiki wa Khristu Yesu kwa anthu amitundu, wakutumikira Uthenga Wabwino wa Mulungu, kuti kupereka kwake kwa anthu amitundu kulandirike, koyeretsedwa ndi Mzimu Woyera.

17Chifukwa chake ndili nacho chodzitamandira cha mu Khristu Yesu ndi zinthu za kwa Mulungu.

18Agal. 2.8Pakuti sindingathe kulimba mtima kulankhula zinthu zimene Khristu sanazichite mwa ine zakumveretsa anthu amitundu, ndi mau ndi ntchito,

19Mac. 19.11mu mphamvu ya zizindikiro ndi zozizwitsa, mu mphamvu ya Mzimu Woyera; kotero kuti ine kuyambira ku Yerusalemu ndi kuzungulirako kufikira ku Iliriko, ndinakwanitsa Uthenga Wabwino wa Khristu;

202Ako. 10.13, 15-16ndipo chotero ndinachiyesa chinthu chaulemu kulalikira Uthenga Wabwino, pamalopo Khristu asanatchulidwe kale, kuti ndisamange nyumba pa maziko a munthu wina.

21Yes. 52.15Koma monga kwalembedwa,

Iwo amene uthenga wake sunawafikire, adzaona,

ndipo iwo amene sanamve, adzadziwitsa.

22 Aro. 1.13 Chifukwa chakenso ndinaletsedwa kawirikawiri kudza kwa inu;

23Mac. 19.21koma tsopano, pamene ndilibe malo m'maiko akuno, ndipo pokhala ndi kulakalaka zaka zambiri kudza kwa inu, ndidzatero,

24pamene paliponse ndidzapita ku Spaniya. Pakuti ndiyembekeza kuonana ndi inu pa ulendo wanga, ndi kuperekezedwa ndi inu panjira panga kumeneko, ngati nditayamba kukhuta pang'ono ndi kukhala ndi inu.

25Mac. 19.21Koma tsopano ndipita ku Yerusalemu, ndilikutumikira oyera mtima.

261Ako. 16.1-2Pakuti kunakondweretsa a ku Masedoniya ndi Akaya kuchereza osauka a kwa oyera mtima a ku Yerusalemu.

27Aro. 11.17; 1Ako. 9.11Pakuti kunakondweretsa iwo; ndiponso iwo ali amangawa ao. Pakuti ngati amitundu anagawana zinthu zao zauzimu, alinso amangawa akutumikira iwo ndi zinthu zathupi.

28Koma pamene ndikatsiriza ichi, ndi kuwasindikizira iwo chipatso ichi, ndidzapyola kwanu kupita ku Spaniya.

29Aro. 1.11Ndipo ndidziwa kuti pamene ndikadza kwanu, ndidzafika m'kudzaza kwake kwa chidalitso cha Khristu.

30 Akol. 4.12 Ndipo ndikudandaulirani, abale, ndi Ambuye wathu Yesu Khristu, ndi chikondi cha Mzimu, kuti mudzalimbike pamodzi ndi ine m'mapemphero anu kwa Mulungu chifukwa cha ine;

31kuti ndikapulumutsidwe kwa osamvera aja a ku Yudeya; ndi kuti utumiki wanga wa ku Yerusalemu ukhale wolandiridwa bwino ndi oyera mtima;

32Aro. 1.10kuti ndi chimwemwe ndikadze kwa inu mwa chifuniro cha Mulungu, ndi kupumula pamodzi ndi inu.

331Ako. 14.33Ndipo Mulungu wa mtendere akhale ndi inu nonse. Amen.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help