LUKA Mau Oyamba - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

Mau OyambaBuku la Luka likunena za Yesu monga Mpulumutsi wolonjezedwa uja wa Aisraele komanso Mpulumutsi wa anthu onse. Luka akunena kuti Yesu anaitanidwa ndi Mzimu wa Ambuye kuti, “awuze anthu osauka Uthenga Wabwino” (4.18), ndipo uthengawo ukuonetsa kuti Yesu anali wokhudzidwa ndi anthu amene ali ndi zosowa zosiyanasiyana. Nkhani inanso imene ikuonekera kwambiri mu buku la Luka ndiyo ya chimwemwe. Makamaka izi zikupezeka mu mitu yoyambirira ya bukuli pamene akunena za kubwera kwa Yesu, komanso kumapeto pamene Yesu akukwera kunka kumwamba. Luka analembanso mbiri ya chiyambi ndi kukula kwa mpingo wa Chikhristu Yesu atakwera mu buku lija la Machitidwe.Bukuli lili ndi magawo awiri (mutu 1—2 ndi 9—19) m'mene muli nkhani zimene zikupezeka mu Luka yekha, nkhanizi ndi monga nyimbo ya angelo ndi ulendo wa abusa kukaona Yesu ali kakhanda, mwana Yesu ali mu Kachisi, ndiponso fanizo la Msamariya wachifundo ndi la Mwana wolowerera. Mu buku lonseli, nkhani yaikulu yagona pa pemphero, Mzimu Woyera, udindo wa azimai pa utumiki wa Yesu komanso kuti Mulungu amakhululukira machimo.Za mkatimuMau oyamba 1.1-4Kubadwa ndi ubwana wa Yohane Mbatizi komanso Yesu 1.5—2.52Utumiki wa Yohane Mbatizi 3.1-20Ubatizo ndi kuyesedwa kwa Yesu 3.21—4.13Utumiki wa Yesu ku Galileya 4.14—9.50Kuchokera ku Galileya kupita ku Yerusalemu 9.51—19.27Sabata yomaliza mu Yerusalemu ndi madera oyandikira 19.28—23.56Kuukanso, kuonekera ndi kukwera kumwamba kwa Ambuye 24.1-53
Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help