1 1Sam. 2.6; Yer. 30.17 Tiyeni, tibwerere kunka kwa Yehova; pakuti wang'amba, nadzatipoletsera; wakantha, nadzatimanga.
2Atapita masiku awiri adzatitsitsimutsa, tsiku lachitatu adzatiutsa; ndipo tidzakhala ndi moyo pamaso pake.
3Yob. 29.23; Yes. 54.13; Yoh. 7.17Tidziwe tsono, tilondole kudziwa Yehova; kutuluka kwake kwakonzekeratu ngati matanda kucha; ndipo adzatidzera ngati mvula, ngati mvula ya masika yakuthirira dziko.
Efuremu ndi Yuda adzudzulidwa4 Hos. 13.3 Efuremu iwe, ndidzakuchitira chiyani? Yuda iwe, ndikuchitire chiyani? Pakuti kukoma mtima kwako kukunga mtambo wam'mawa ndi ngati mame akuphawa mamawa.
5Chifukwa chake ndawalikha mwa aneneri; ndawapha ndi mau a pakamwa panga; ndi maweruzo anga atuluka ngati kuunika.
61Sam. 15.22; Mas. 50.8-9; Mat. 9.13; 12.7; Yoh. 17.3Pakuti ndikondwera nacho chifundo, si nsembe ai; ndi kumdziwa Mulungu kuposa nsembe zopsereza.
7Koma iwo analakwira chipangano ngati Adamu, m'mene anandichitira monyenga.
8Giliyadi ndiwo mzinda wa ochita zoipa, wa mapazi a mwazi.
9Hos. 5.1-2Ndipo monga magulu a mbala alalira munthu, momwemo msonkhano wa ansembe amapha panjira ya ku Sekemu; indedi achita choipitsitsa.
10Yer. 5.30-31M'nyumba ya Israele ndinaona chinthu choopsetsa; pamenepo pali uhule wa Efuremu; Israele wadetsedwa.
11Yer. 51.33Akuikidwiratunso nyengo yakukolola, Yuda iwe, pamene ndikabwezanso undende wa anthu anga.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.