1Ndipo likasa la Yehova linakhala ku dziko la Afilisti miyezi isanu ndi iwiri.
2Gen. 41.8; Eks. 7.11Ndipo Afilistiwo anaitana ansembe ndi oombeza, nati, Tichitenji ndi likasa la Yehova? Mutidziwitse chimene tilitumize nacho kumalo kwake.
3Ndipo iwo anati, Ngati mulitumiza kwina likasa la Mulungu wa Israele, musalitumize lopanda kanthu; koma makamaka mulibweze ndi nsembe yopalamula, mukatero mudzachiritsidwa, ndi kudziwa chifukwa chake dzanja lake lili pa inu losachoka.
41Sam. 6.17-18Ndipo iwo aja anati, Tidzambwezera nsembe yopalamula yanji? Ndipo iwo anati, Mafundo asanu agolide, ndi mbewa zisanu zagolide, monga mwa chiwerengo cha mafumu a Afilisti; popeza kusauka kumodzi kunali pa inu nonse, ndi pa mafumu anu.
5Yos. 7.19; Mas. 22.23Chifukwa chake muzipanga zifanizo za mafundo anu, ndi zifanizo za mbewa zanu zimene ziipitsa dziko; ndipo muchitire ulemu Mulungu wa Israele; kuti kapena adzaleza dzanja lake pa inu, ndi pa milungu yanu, ndi padziko lanu.
6Eks. 7.13; 8.15; 14.17Mulikuumitsiranji mitima yanu, monga Aejipito ndi Farao anaumitsa mitima yao? Kodi iwo sanalole anthuwo amuke, Iye atachita kodabwitsa pakati pao, ndipo anamuka?
72Sam. 6.3Chifukwa chake tsono, tengani, nimukonze galeta latsopano, ndi ng'ombe ziwiri zamkaka, zosalawa goli chikhalire, ndipo mumange ng'ombezo pagaleta, muzichotsere ana ao kunka nao kwanu;
81Sam. 6.4-5ndipo mutenge likasa la Yehova, nimuliike pagaletapo; nimuike zokometsera zagolide, zimene muzipereka kwa Iye ngati nsembe yopalamula, m'bokosi pambali pake; nimulitumize lichoke.
9Ndipo muyang'anire, ngati likwera panjira ya malire akeake ku Betesemesi, Iye anatichitira choipa ichi chachikulu; koma likapanda kutero, tidzadziwapo kuti dzanja limene linatikantha, silili lake; langotigwera tsokali.
10Ndipo anthuwo anatero; natenga ng'ombe ziwiri zamkaka, nazimanga pagaleta, natsekera anao kwao;
11naika likasa la Yehova pagaletapo, ndi bokosi m'mene munali mbewa zagolide ndi zifanizo za mafundo ao.
12Ndipo ng'ombezo zinatsata njira yolunjika ku Betesemesi, zinali kuyenda mumseu, zilikulira; sizinapatukire ku dzanja lamanja, kapena kulamanzere; ndipo mafumu a Afilisti anazitsatira kufikira ku malire a Betesemesi.
13Ndipo a ku Betesemesi analikumweta tirigu wao m'chigwamo; natukula maso ao, naona likasalo, nakondwera pakuliona.
14Ndipo galetalo linafika m'munda wa Yoswa wa ku Betesemesi, ndi kuima momwemo, pamwala waukulu; ndipo anawaza matabwa a galetalo, nazipereka ng'ombezo nsembe yopsereza kwa Yehova.
15Ndipo Alevi anatsitsa likasa la Yehova, ndi bokosi linali nalo, m'mene munali zokometsera zagolide, naziika pamwala waukuluwo; ndipo anthu a ku Betesemesi anapereka nsembe zopsereza, naphera nsembe kwa Yehova tsiku lomwelo.
16Yos. 13.3Ndipo pamene mafumu asanu a Afilisti anaonerako, anabwerera kunka ku Ekeroni tsiku lomwelo.
171Sam. 6.4Ndipo amenewa ndiwo mafundo agolide amene Afilisti anabwezera kwa Yehova akhale nsembe yopalamula, kwa Asidodi limodzi, kwa Gaza limodzi, kwa Asikeloni limodzi, kwa Gati limodzi, kwa Ekeroni limodzi;
18ndiponso mbewa zagolide, monga chiwerengo cha midzi yonse ya mafumu asanu a Afilisti, mizinda ya malinga, ndi midzi yopanda malinga; kufikira ku mwala waukulu, adaikapo likasa la Yehova; mwalawo ulipobe kufikira lero m'munda wa Yoswa wa ku Betesemesi.
19Eks. 19.21; Num. 4.5, 15, 20Ndipo Mulungu anakantha anthu a ku Betesemesi, chifukwa anasuzumira m'likasa la Yehova, anakantha anthu zikwi makumi asanu; ndipo anthu analira maliro, chifukwa Yehova anawakantha anthuwo ndi makanthidwe aakulu.
Likasa lisungidwa ku Kiriyati-Yearimu20 2Sam. 6; Mala. 3.2 Ndipo a ku Betesemesi anati, Akhoza ndani kuima pamaso pa Yehova, Mulungu Woyera uyu? Ndipo adzakwera kwa yani pakutichokera ife?
211Mbi. 13.5-6Ndipo anatumiza mithenga kwa anthu a ku Kiriyati-Yearimu, nati, Afilisti anabwera nalo likasa la Yehova, mutsike; ndi kukwera nalo kwanu.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.