MASALIMO 135 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

Mulungu alemekezedwa pa ukulu wake. Mafano ndi achabe

1 Aleluya; Lemekezani dzina la Yehova!

Lemekezani inu atumiki a Yehova.

2 Luk. 2.37 Inu akuimirira m'nyumba ya Yehova,

m'mabwalo a nyumba ya Mulungu wathu.

3 Mas. 119.68 Lemekezani Yehova; pakuti Yehova ndiye wabwino;

muimbire zolemekeza dzina lake; pakuti nkokondweretsa kutero.

4 Eks. 19.5 Pakuti Yehova anadzisankhira Yakobo,

Israele, akhale chuma chake chenicheni.

5Pakuti ndidziwa kuti Yehova ndi wamkulu,

ndi Ambuye wathu aposa milungu yonse.

6 Mas. 115.3 Chilichonse chimkonda Yehova achichita,

kumwamba ndi padziko lapansi, m'nyanja ndi mozama monse.

7Akweza mitambo ichokere ku malekezero a dziko lapansi;

ang'animitsa mphezi zidzetse mvula;

atulutsa mphepo mosungira mwake.

8 Eks. 12.12, 29 Anapanda oyamba a Ejipito,

kuyambira munthu kufikira zoweta.

9 Eks. 7.10 Anatumiza zizindikiro ndi zodabwitsa pakati pako, Ejipito iwe,

pa Farao ndi pa omtumikira onse.

10 Num. 21.24-35 Ndiye amene anapanda amitundu ambiri,

napha mafumu amphamvu;

11Sihoni mfumu ya Aamori,

ndi Ogi mfumu ya Basani,

ndi maufumu onse a Kanani:

12Ndipo anapereka dziko lao likhale cholowa,

cholowa cha kwa Israele anthu ake.

13 Eks. 3.15 Dzina lanu, Yehova, likhala kosatha;

chikumbukiro chanu, Yehova, kufikira mibadwomibadwo.

14 Deut. 32.36 Pakuti Yehova adzaweruza anthu ake,

koma adzaleka atumiki ake.

15 Mas. 115.4-10 Mafano a amitundu ndiwo siliva ndi golide,

ntchito ya manja a anthu.

16Pakamwa ali napo koma osalankhula;

maso ali nao, koma osapenya;

17makutu ali nao, koma osamva;

inde, pakamwa pao palibe mpweya.

18Akuwapanga adzafanana nao;

inde, onse akuwakhulupirira.

19A nyumba ya Israele inu, lemekezani Yehova:

A nyumba ya Aroni inu, lemekezani Yehova:

20A nyumba ya Levi inu, lemekezani Yehova:

Inu akuopa Yehova, lemekezani Yehova.

21Alemekezedwe Yehova kuchokera mu Ziyoni,

amene akhala mu Yerusalemu.

Aleluya.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help