1 Eks. 9.29; 1Ako. 10.26, 28 Dziko lapansi nla Yehova ndi zodzala zake zomwe,
dziko lokhalamo anthu ndi iwo okhala m'mwemo.
2Pakuti Iye analimanga pazinyanja,
nalikhazika pamadzi.
3 Mas. 15.1-5 Adzakwera ndani m'phiri la Yehova?
Nadzaima m'malo ake oyera ndani?
4 Yes. 33.15-16; Mat. 5.8 Woyera m'manja, ndi woona m'mtima, ndiye;
iye amene sanakweze moyo wake kutsata zachabe,
ndipo salumbira monyenga.
5Iye adzalandira dalitso kwa Yehova,
ndi chilungamo kwa Mulungu wa chipulumutso chake.
6Uwu ndi mbadwo wa iwo akufuna Iye,
iwo akufuna nkhope yanu, Mulungu wa Yakobo.
7 Mas. 118.19-20; Yes. 26.2; Hag. 2.7; Mala. 3.1 Weramutsani mitu yanu, zipata inu;
ndipo kwezekani inu, zitseko zosatha,
kuti Mfumu ya ulemerero ilowe.
8Mfumu imene ya ulemerero ndani?
Yehova wamphamvu ndi wolimba,
Yehova wolimba kunkhondo.
9Weramutsani mitu yanu, zipata inu;
inde weramutsani, zitseko zosatha inu,
kuti Mfumu ya ulemerero ilowe.
10Mfumu imene ya ulemerero ndani?
Yehova wa makamumakamu,
ndiye Mfumu ya ulemerero.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.