MARKO 7 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

Miyambo ya makolo ao(Mat. 15.1-20)

1Ndipo anasonkhana kwa Iye Afarisi, ndi alembi ena, akuchokera ku Yerusalemu,

2ndipo anaona kuti ophunzira ake ena anadya mkate ndi m'manja mwakuda, ndiwo osasamba.

3Pakuti Afarisi, ndi Ayuda onse sakudya osasamba m'manja ao, kuti asungire mwambo wa akulu;

4ndipo pakuchoka kumsika, sakudya osasamba m'thupi; ndipo zilipo zinthu zina zambiri anazilandira kuzisunga, ndizo matsukidwe a zikho, ndi miphika, ndi zotengera zamkuwa.

5

17Mat. 15.15Ndipo m'mene Iye adalowa m'nyumba kusiyana ndi khamulo, ophunzira ake anamfunsa Iye fanizolo.

18Ndipo ananena nao, Mutero inunso opanda nzeru kodi? Kodi simuzindikira kuti kanthu kalikonse kochokera kunja kukalowa mwa munthu, sikangathe kumdetsa iye;

19chifukwa sikalowa mumtima mwake, koma m'mimba mwake, ndipo katulukira kuthengo? Ndipo potero anayeretsa zakudya zonse.

20Ndipo anati, Chotuluka mwa munthu ndicho chidetsa munthu.

21Gen. 6.5; 8.21; Mat. 15.8Pakuti m'kati mwake mwa mitima ya anthu, mutuluka maganizo oipa, zachiwerewere,

22zakuba, zakupha, zachigololo, masiriro, zoipa, chinyengo, chinyanso, diso loipa, mwano, kudzikuza, kupusa:

23zoipa izi zonse zituluka m'kati, nkudetsa munthu.

Mkazi wa Siro-Fenisiya(Mat. 15.21-28)

24Ndipo Iye anauka nachoka kumeneko, nanka ku maiko a ku Tiro ndi Sidoni. Ndipo analowa m'nyumba, nafuna kuti asadziwe anthu; ndipo sanakhoze kubisika.

25Koma pomwepo mkazi, kabuthu kake kanali ndi mzimu wonyansa, pamene anamva za Iye, anadza, nagwa pa mapazi ake.

26Koma mkaziyo anali Mgriki, mtundu wake Msiro-Fenisiya. Ndipo anampempha Iye kuti atulutse chiwanda m'mwana wake.

27Ndipo ananena naye, Baleka, ayambe akhuta ana; pakuti si kwabwino kuti titenge mkate wa ana, ndi kuutayira tiagalu.

28Koma iye anavomera nanena ndi Iye, Inde Ambuye; tingakhale tiagalu ta pansi pa gome tikudyako nyenyeswa za ana.

29Ndipo anati kwa iye, Chifukwa cha mau amene, muka; chiwanda chatuluka m'mwana wako wamkazi.

30Ndipo anachoka kunka kunyumba kwake, napeza mwana atamgoneka pakama, ndi chiwanda chitatuluka.

Yesu achiritsa munthu wogontha ndi wosalankhula

31 Mat. 15.29 Ndipo anatulukanso m'maiko a ku Tiro, nadzera pakati pa Sidoni, kufikira ku nyanja ya Galileya, ndi kupyola pakati pa maiko a ku Dekapoli.

32Ndipo anadza naye kwa Iye munthu wogontha, ndi wachibwibwi; ndipo anampempha Iye kuti aike dzanja pa iye.

33Mrk. 8.23; Yoh. 9.6Ndipo anampatula pa khamu la anthu pa yekha, nalonga zala zake m'makutu mwake, nalavula malovu, nakhudza lilime lake:

34Yoh. 11.33, 38nagadamira kumwamba, nausa moyo, nanena naye, Efata, ndiko, Tatseguka.

35Yes. 35.5-6Ndipo makutu ake anatseguka, ndi chomangira lilime lake chinamasulidwa, ndipo analankhula chilunjikire.

36Mrk. 5.43Ndipo anawalamulira kuti asauze munthu aliyense; koma monga momwe Iye anawalamulitsa momwenso makamaka analalikira kopambana.

37Ndipo anadabwa kwakukulukulu, nanena, Wachita Iye zonse bwino; angakhale ogontha awamvetsa, ndi osalankhula awalankhulitsa.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help