2 MBIRI 22 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

Ahaziya mfumu ya Yuda aphedwa ndi Yehu(2Maf. 8.25-29; 9.21-28)

1 2Maf. 8.24-29 Ndipo okhala mu Yerusalemu anamlonga Ahaziya mwana wake wamng'ono akhale mfumu m'malo mwake; pakuti gulu la anthu, adadzawo pamodzi ndi Aarabu kuchigono, adapha ana oyamba onse. Momwemo Ahaziya mwana wa Yehoramu anakhala mfumu ya Yuda.

2Ahaziya anali wa zaka makumi anai mphambu ziwiri polowa ufumu wake, nakhala mfumu mu Yerusalemu chaka chimodzi; ndi dzina la make ndiye Ataliya mwana wa Omuri.

3Iyenso anayenda m'njira za nyumba ya Ahabu; pakuti wompangira ndi make achite choipa.

4Ndipo anachita choipa pamaso pa Yehova, monga umo anachitira a nyumba ya Ahabu; pakuti ompangira ndi iwowa, atamwalira atate wake; ndi kuonongeka kwake nkumeneko.

5Anayendanso m'kupangira kwao, namuka pamodzi ndi Yehoramu mwana wa Ahabu mfumu ya Israele, kukayambana nkhondo ndi Hazaele mfumu ya Aramu ku Ramoti Giliyadi; ndipo Aaramu anamlasa Yehoramu.

6Nabwerera iye kuti amchize ku Yezireele, apole mabala amene adamkantha ku Rama, pamene anayambana ndi Hazaele mfumu ya Aramu. Ndipo Ahaziya mwana wa Yehoramu mfumu ya Yuda anatsikira kukaona Yehoramu mwana wa Ahabu mu Yezireele, popeza anadwala.

71Maf. 12.5; 2Maf. 9.6-7Kuonongeka kwa Ahaziya tsono nkwa Mulungu, kuti amuke kwa Yehoramu; pakuti atafika anatulukira pamodzi ndi Yehoramu kukayambana ndi Yehu mwana wa Nimisi, amene Yehova anamdzoza alikhe nyumba ya Ahabu.

82Maf. 10.11-14Ndipo kunali, pakulanga Yehu nyumba ya Ahabu, anapeza akalonga a Yuda, ndi ana a abale a Ahaziya, akutumikira Ahaziya, nawapha.

92Maf. 9.27-28; 2Mbi. 17.4Atatero, anafunafuna Ahaziya, namgwira alikubisala mu Samariya, nabwera naye kwa Yehu, namupha; ndipo anamuika; pakuti anati, Ndiye mwana wa Yehosafati, wofuna Yehova ndi mtima wake wonse. Ndipo panalibe wina wa nyumba ya Ahaziya wa mphamvu yakusunga ufumuwo.

Ataliya apha achifumu onse, Yowasi apulumuka(2Maf. 11.1-3)

10 2Maf. 11.1-3 Pamene Ataliya mai wake wa Ahaziya anaona kuti mwana wake adafa, anauka, naononga mbeu yonse yachifumu ya nyumba ya Yuda.

11Koma Yehoseba mwana wamkazi wa mfumu anatenga Yowasi mwana wa Ahaziya, namuba pakati pa ana a mfumu ophedwa, namlonga iye ndi mlezi wake m'chipinda chogonamo. Momwemo Yehoseba mwana wamkazi wa mfumu Yehoramu, mkazi wa Yehoyada wansembe (popeza ndiye mlongo wake wa Ahaziya), anambisira Ataliya, angamuphe.

12Ndipo iye anali nao wobisika m'nyumba ya Mulungu zaka zisanu ndi chimodzi; nakhala Ataliya mfumu yaikazi ya dziko.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help