1 Yes. 43.25; 44.22; Akol. 2.14 Mundichitire ine chifundo, Mulungu,
monga mwa kukoma mtima kwanu;
monga mwa unyinji wa nsoni zanu zokoma
mufafanize machimo anga.
2 Yes. 1.16; 1Yoh. 1.7, 9 Mubwereze kunditsuka mphulupulu yanga,
ndipo mundiyeretse kundichotsera choipa changa.
3 Mas. 32.5 Chifukwa ndazindikira machimo anga;
ndipo choipa changa chili pamaso panga chikhalire.
4 Gen. 39.9; 2Sam. 12.13; Aro. 3.4 Pa Inu, Inu nokha, ndinachimwa,
ndipo ndinachichita choipacho pamaso panu;
kuti mukhale wolungama pakulankhula Inu,
mukhalenso woyera pa kuweruza kwanu.
5 Yob. 14.4; Aro. 5.12 Onani, ndinabadwa m'mphulupulu,
ndipo mai wanga anandilandira m'zoipa.
6 Yob. 38.36 Onani, Inu mukondwera ndi zoonadi m'malo a m'katimo;
ndipo m'malo a m'tseri mudzandidziwitsa nzeru.
7 Num. 19.18; Yes. 1.18 Mundiyeretse ndi hisope ndipo ndidzayera;
munditsuke ndipo ndidzakhala wa mbuu woposa matalala.
8Mundimvetse chimwemwe ndi kusekera,
kuti mafupawo munawathyola akondwere.
9 Yer. 16.17 Muzibisire nkhope yanu zolakwa zanga,
ndipo mufafanize mphulupulu zanga zonse.
10 Ezk. 11.19; 36.25-26; Aef. 4.23-24 Mundilengere mtima woyera, Mulungu;
mukonze mzimu wokhazikika m'kati mwanga.
11 Aro. 8.9; Aef. 4.30 Musanditaye kundichotsa pamaso panu;
musandichotsere Mzimu wanu Woyera.
12 2Ako. 3.17 Mundibwezere chimwemwe cha chipulumutso chanu;
ndipo mzimu wakulola undigwirizize.
13Pomwepo ndidzalangiza ochimwa njira zanu;
ndipo olakwa adzabwera kwa Inu.
14 2Sam. 11.15, 17; 12.9 Mundilanditse kumlandu wa mwazi, Mulungu,
ndinu Mulungu wa chipulumutso changa;
lilime langa lidzakweza nyimbo ya chilungamo chanu.
15Ambuye, tsegulani pa milomo yanga;
ndipo pakamwa panga padzalalikira ulemekezo wanu.
16 Mas. 50.8 Pakuti simukondwera ndi nsembe, mwenzi nditapereka;
nsembe yopsereza simuikonda.
17 Mas. 34.18; Yes. 57.15 Nsembe za Mulungu ndizo mzimu wosweka;
Inu, Mulungu, simudzaupeputsa mtima wosweka ndi wolapa.
18Chitirani Ziyoni chokoma monga mwa kukondwera kwanu;
mumange malinga a miyala a Yerusalemu.
19 Mala. 3.3 Pamenepo mudzakondwera nazo nsembe zachilungamo,
ndi nsembe yopsereza ndi yopsereza yathunthu;
pamenepo adzapereka
ng'ombe paguwa lanu la nsembe.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.