NYIMBO YA SOLOMONI 4 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

Mkwati alemekeza mkwatibwi

1Taona, wakongola, bwenzi langa,

namwaliwe, taona, wakongola;

maso ako akunga a nkhunda patseri pa chophimba chako.

Tsitsi lako likunga gulu la mbuzi,

zooneka paphiri la Giliyadi.

2Mano ako akunga gulu la nkhosa zosengasenga,

zokwera kuchokera kosamba;

yonse ili ndi ana awiri,

palibe imodzi yopoloza.

3Milomo yako ikunga mbota yofiira,

m'kamwa mwako ndi kukoma:

Palitsipa pako pakunga phande la khangaza

paseri pa chophimba chako.

4 Neh. 3.19 Khosi lako likunga nsanja ya Davide anaimangira zida,

apachikapo zikopa zikwi,

ngakhale zikopa zonse za amuna amphamvu.

5Mawere ako awiri akunga ana awiri a nswala obadwa limodzi,

akudya pakati pa akakombo.

6Mpaka dzuwa litapepa, mithunzi ndi kutanimpha,

ndikamuka kuphiri la mure,

ndi kuchitunda cha lubani.

7 Aef. 5.27 Wakongola monsemonse, wokondedwa wanga, namwaliwe,

mulibe chilema mwa iwe.

8Idza nane kuchokera ku Lebanoni, mkwatibwi,

kuchokera nane ku Lebanoni:

Unguza pamwamba pa Amana,

pansonga ya Seniri ndi Heremoni,

pa ngaka za mikango,

pa mapiri a anyalugwe.

9Walanda mtima wanga, mlongo wanga, mkwatibwi;

walanda mtima wanga ndi diso lako limodzi,

ndi chinganga chimodzi cha pakhosi pako.

10Ha, chikondi chako nchokongola, mlongo wanga, mkwatibwi!

Kodi chikondi chako sichiposa vinyo?

Kununkhira kwa mphoka yako

ndi kuposa zonunkhiritsa za mitundumitundu!

11 Hos. 14.6-7 M'milomo yako, mkwatibwi, mukukha uchi,

uchi ndi mkaka zili pansi pa lilime lako;

kununkhira kwa zovala zako

ndi kunga kununkhira kwa Lebanoni.

12Mlongo wanga, mkwatibwi ndiye munda wotsekedwa;

ngati kasupe wotsekedwa, ndi chitsime chopikiza.

13Mphukira zako ndi munda wamakangaza,

ndi zipatso zofunika, bonongwe ndi narido.

14Narido ndi chikasu,

nzimbe ndi sinamoni, ndi mitengo yonse ya lubani;

mure ndi khonje, ndi zonunkhiritsa zonse zomveka.

15 Yes. 49.10; Yoh. 4.10 Ndiwe kasupe wa m'minda,

chitsime cha madzi amoyo,

ndi mitsinje yoyenda yochokera ku Lebanoni.

Ayankha mkwatibwi

16Galamuka, mphepo ya kumpoto iwe,

nudze, mphepo iwe ya kumwera;

nuombe pamunda panga, kuti zonunkhiritsa zake zitulukemo.

Bwenzi langa mnyamatayo, alowe m'munda mwake,

nadye zipatso zake zofunika.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help