MIYAMBO 22 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

1 Mlal. 7.1 Mbiri yabwino ifunika kopambana chuma chambiri;

kukukomera mtima anzako kuposa siliva ndi golide.

2 1Ako. 12.21 Wolemera ndi wosauka akumana,

wolenga onsewo ndiye Yehova.

3Wochenjera aona zoipa, nabisala;

koma achibwana angopitirira, nalipitsidwa.

4 Mat. 6.33 Mphotho ya chifatso ndi kuopa Yehova

ndiye chuma, ndi ulemu, ndi moyo.

5 1Yoh. 5.18 Minga ndi misampha ili m'njira ya wokhota;

koma wosunga moyo wake adzatalikira imeneyo.

6 Aef. 6.4 Phunzitsa mwana poyamba njira yake;

ndipo angakhale atakalamba sadzachokamo.

7 Yak. 2.6 Wolemera alamulira osauka;

ndipo wokongola ndiye kapolo wa womkongoletsa.

8 Yob. 4.8; Hos. 10.13 Wofesa zosalungama adzakolola tsoka;

ndipo nthyole ya mkwiyo wake idzalephera.

9 2Ako. 9.6 Mwini diso lamataya adzadala;

pakuti apatsa osauka zakudya zake.

10 Gen. 21.9-10 Ukainga wonyoza, makangano adzatuluka;

makani ndi manyazi adzalekeka.

11Wokonda kuyera mtima,

mfumu idzakhala bwenzi lake

chifukwa cha chisomo cha milomo yake.

12Maso a Yehova atchinjiriza wodziwa;

koma agwetsa mau a munthu wa ziwembu.

13Waulesi ati, Pali mkango panjapo,

ndidzaphedwa pamakwalalapo.

14M'kamwa mwa mkazi wachiwerewere muli dzenje lakuya;

yemwe Yehova amkwiyira adzagwamo.

15Utsiru umangidwa mumtima mwa mwana;

koma nthyole yomlangira idzauingitsira kutali.

16Wotsendereza waumphawi kuti achulukitse chuma chake,

ndi wopatsa wolemera kanthu, angosauka.

Malangizo a pa makhalidwe oyenera munthu

17Tchera makutu ako, numvere mau a anzeru,

nulozetse mtima wako kukadziwa zanga.

18Pakuti mauwo akondweretsa ngati uwasunga m'kati mwako,

ngati akhazikika pamodzi pa milomo yako.

19Ndakudziwitsa amenewo lero, ngakhale iwedi,

kuti ukhulupirire Yehova.

20Kodi sindinakulembere zoposa

za uphungu ndi nzeru;

21kuti ukadziwitse ntheradi yake ya mau oona,

nukabwere ndi mau oona kwa iwo amene anakutumiza?

22 Eks. 23.6; Zek. 7.10 Usalande za waumphawi chifukwa ali waumphawi,

ngakhale kutsendereza wosauka kubwalo.

23 1Sam. 24.12; 25.39; Yer. 51.36 Pakuti Yehova adzanenera mlandu wao;

omwe akwatula zao Iye adzakwatula moyo wao.

24Usayanjane ndi munthu wokwiya msanga;

ngakhale kupita ndi mwamuna waukali;

25kuti ungaphunzire mayendedwe ake,

ndi kutengera moyo wako msampha.

26Usakhale wodulirana mpherere,

ngakhale kumperekera chikole cha ngongole zake.

27Ngati ulibe chobwezera

kodi achotserenji kama lako pansi pako?

28 Deut. 19.14 Usasunthe chidziwitso chakale cha m'malire,

chimene makolo ako anachiimika.

29Kodi upenya munthu wofulumiza ntchito zake?

Adzaima pamaso pa mafumu, osaima pamaso pa anthu achabe.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help