1Pamenepo Yona anapemphera kwa Yehova Mulungu wake ali m'mimba mwa nsombayo.
2Mas. 120.1Ndipo anati,
Ndinaitana Yehova m'nsautso wanga,
ndipo anandiyankha ine;
ndinafuula ndili m'mimba ya manda,
ndipo munamva mau anga.
3 Mas. 42.7; 88.6 Pakuti munandiponya mwakuya m'kati mwa nyanja,
ndipo madzi anandizinga;
mafunde anu onse a nyondonyondo anandimiza.
4Ndipo ndinati, Ndatayika ndichoke pamaso panu;
koma ndidzapenyanso Kachisi wanu wopatulika.
5 Mas. 69.1 Madzi anandizinga mpaka moyo wanga,
madzi akuya anandizungulira,
kayandeyande wa m'nyanja anandikulunga mutu.
6 Mas. 16.10 Ndinatsikira kumatsinde a mapiri,
mipingiridzo ya dziko inanditsekereza kosatha;
koma munandikwezera moyo wanga
kuuchotsa kuchionongeko, Yehova Mulungu wanga.
7 Mas. 18.6 Pokomoka moyo wanga m'kati mwanga ndinakumbukira Yehova;
ndi pemphero langa linafikira Inu mu Kachisi wanu wopatulika.
8Iwo osamalira mabodza opanda pake
ataya chifundo chaochao.
9 Mas. 3.8; 116.17-18 Koma ine ndidzakupherani Inu nsembe ndi mau akuyamika,
ndidzakwaniritsa chowinda changa.
Chipulumutso ncha Yehova.
10Pamenepo Yehova analankhula ndi nsombayo, ndipo inamsanzira Yona kumtunda.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.