1 ATESALONIKA 4 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

Atsate kuyeramtima, chikondano, ndi khama

1 Akol. 1.10 Chotsalira tsono, abale, tikupemphani ndi kukudandaulirani mwa Ambuye Yesu, kuti, monga munalandira kwa ife mayendedwe okoma, muyenera kuyendanso ndi kukondweretsa Mulungu, monganso mumayenda, chulukani koposa momwemo.

2Pakuti mudziwa malangizo amene tinakupatsani mwa Ambuye Yesu.

3Aef. 5.17, 27Pakuti ichi ndi chifuniro cha Mulungu, chiyeretso chanu, kuti mudzipatule kudama;

4Aro. 6.19yense wa inu adziwe kukhala nacho chotengera chake m'chiyeretso ndi ulemu,

5Akol. 3.5kosati m'chisiriro cha chilakolako chonyansa, monganso amitundu osadziwa Mulungu;

6Lev. 19.11, 13; 2Ate. 1.8asapitirireko munthu, nanyenge mbale wake m'menemo, chifukwa Ambuye ndiye wobwezera wa izi zonse, monganso tinakuuziranitu, ndipo tinachitapo umboni.

7Aheb. 12.14; 1Pet. 1.15Pakuti Mulungu sanaitane ife titsate chidetso, koma chiyeretso.

8Luk. 10.16; 1Ako. 2.10Chifukwa chake iye wotaya ichi, sataya munthu, komatu Mulungu, wakupatsa Mzimu wake Woyera kwa inu.

9 Yoh. 14.26; 1Yoh. 3.11, 23 Koma kunena za chikondano cha pa abale sikufunika kuti akulembereni; pakuti wakukuphunzitsani ndi Mulungu, kuti mukondane wina ndi mnzake;

101Ate. 1.7; 3.12pakutinso munawachitira ichi abale onse a mu Masedoniya yense. Koma tikudandaulirani, abale, muchulukireko koposa,

112Ate. 3.11-12ndi kuti muyesetse kukhala chete ndi kuchita za inu eni ndi kugwira ntchito ndi manja anu, monga tinakuuzani;

122Ako. 8.21kuti mukayende oona mtima pa iwo a kunja, ndi kukhala osasowa kanthu.

Za kuuka kwa akufa ndi kubwera kwa Yesu

13 Aef. 2.12 Koma sitifuna, abale, kuti mukhale osadziwa za iwo akugona; kuti mungalire monganso otsalawo, amene alibe chiyembekezo.

141Ako. 15.13-23Pakuti ngati tikhulupirira kuti Yesu adamwalira, nauka, koteronso Mulungu adzatenga pamodzi ndi Iye iwo akugona mwa Yesu.

151Ako. 15.51Pakuti ichi tinena kwa inu m'mau a Ambuye, kuti ife okhala ndi moyo, otsalira kufikira kufikanso kwa Ambuye, sitidzatsogolera ogonawo.

16Mat. 24.30-31; 1Ako. 15.23, 52Pakuti Ambuye adzatsika Kumwamba mwini yekha ndi mfuu, ndi mau a mngelo wamkulu, ndi lipenga la Mulungu; ndipo akufa mwa Khristu adzayamba kuuka;

17Yoh. 12.26; 1Ako. 15.51pamenepo ife okhala ndi moyo, otsalafe, tidzakwatulidwa nao pamodzi m'mitambo, kukakomana ndi Ambuye mumlengalenga, ndipo potero tidzakhala ndi Ambuye nthawi zonse.

18Chomwecho, tonthozanani ndi mau awa.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help