1 Mas. 147.1 Yehova achita ufumu; wadziveka ndi ukulu;
wadziveka Yehova, wadzimangirira mphamvu m'chuuno;
dziko lomwe lokhalamo anthu likhakizika, silidzagwedezeka.
2 Mas. 45.6 Mpando wachifumu wanu ukhazikika kuyambira kale lija;
Inu ndinu wosayambira ndi kale lomwe.
3Mitsinje ikweza, Yehova,
mitsinje ikweza mkokomo wao;
mitsinje ikweza mafunde ao.
4 Mas. 65.7; 89.9 Yehova Wam'mwamba ndiye wamphamvu,
wakuposa mkokomo wa madzi ambiri,
ndi mafunde olimba a nyanja.
5Mboni zanu zivomerezeka ndithu;
chiyero chiyenera nyumba yanu,
Yehova, kunthawi za muyaya.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.