YOBU 8 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

Poona tsoka lao Bilidadi akuti Yobu ndi ana ake anachimwa, anena mofanizira

1Pamenepo anayankha Bilidadi Msuki, nati,

2Udzanena izi kufikira liti?

Ndipo mau a pakamwa pako

adzakhala ngati namondwe kufikira liti?

3 Gen. 18.25; Aro. 3.5 Ngati Mulungu akhotetsa chiweruzo?

Ngati Wamphamvuyonse akhotetsa mlandu?

4Chinkana ana ako anamchimwira Iye,

ndipo anawapereka mwa kulakwa kwao;

5koma ukafunitsitsa Mulungu,

ndi kupembedza Wamphamvuyonse;

6ukakhala woyera ndi woongoka mtima,

zoonadi adzakugalamukira tsopano,

ndi kupindulitsa pokhala pako polungama.

7Ndipo chinkana chiyambi chako chinali chaching'ono,

chitsiriziro chako chidzachuluka kwambiri.

8 Deut. 4.29-32 Pakuti ufunsire tsono mbadwo wapitawo,

nusamalire zimene makolo ao adazisanthula.

9 Mas. 39.5 Pakuti ife ndife adzulo, osadziwa kanthu,

popeza masiku athu a padziko lapansi ndiwo ngati mthunzi;

10amene aja sangakuphunzitse, ndi kukufotokozera,

ndi kutulutsa mau a mumtima mwao?

11Ngati gumbwa aphuka popanda chinyontho?

Ngati manchedza amera popanda madzi?

12Akali auwisi, sanawacheke,

auma, asanaume mathengo onse ena.

13 Mas. 112.10 Momwemo mayendedwe a onse oiwala Mulungu;

ndi chiyembekezo cha onyoza Mulungu; chidzatayika.

14Kulimbika mtima kwake kudzathyoka,

chikhulupiriro chake chikunga nyumba ya kangaude.

15Adzatsamira nyumba yake, koma yosamlimbira;

adzaiumirira koma yosakhalitsa.

16Akhala wamuwisi pali dzuwa,

ndi nthambi zake zitulukira pamunda pake.

17Mizu yake iyangayanga pa kasupe wamadzi,

apenyerera pokhalapo miyala.

18Akamuononga kumchotsa pamalo pake,

padzamkana, ndi kuti, Sindinakuone.

19Taona, ichi ndicho chomkondweretsa panjira pake,

ndi panthaka padzamera ena.

20Taona, Mulungu sakana munthu wangwiro;

kapena kugwiriziza ochita zoipa.

21Koma adzadzaza m'kamwa mwako ndi kuseka,

ndi milomo yako kufuula.

22 Mas. 35.26 Iwo akudana nawe adzavala manyazi;

ndi hema wa oipa adzakhala kuli zii.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help