1Koma Yobu anayankha, nati,
2Mwenzi atayesa bwino chisoni changa,
ndi kuika matsoka anga pamodzi pamuyeso!
3Pakuti zikadalemera tsopano koposa mchenga wa kunyanja;
chifukwa chake mau anga ndasonthokera kunena.
4 Mas. 38.2 Pakuti mivi ya Wamphamvuyonse yandilowa,
mzimu wanga uwumwa ulembe wake;
zoopsa za Mulungu zindindandira nkhondo.
5Kodi mbidzi ilira pokhala nao msipu?
Ilira kodi ng'ombe pa chakudya chake?
6Kodi chinthu chosakolera chidyeka chopanda mchere?
Choyera cha dzira chikolera kodi?
7Zimene moyo wanga ukana kuzikhudza
zikunga chakudya chosakolera kwa ine.
8Ha! Ndikadakhala nacho chimene ndichipempha,
Mulungu akadandipatsa chimene ndichilira!
9 1Maf. 19.4 Chimkomere Mulungu kundiphwanya,
alole dzanja lake lindilikhe!
10 Mac. 20.20 Pamenepo ndidzasangalala,
ndidzakondwera nacho chowawa chosandileka;
pakuti sindinawabise mau a Woyerayo.
11Mphamvu yanga njotani kuti ndiyembekeze?
Mathedwe anga ndi otani kuti ndipirire?
12Kodi mphamvu yanga ndiyo mphamvu ya miyala?
Mnofu wanga ndi mkuwa kodi?
13Mulibe thandizo mwa ine ndekha; chipulumutso chandithawa.
14 Miy. 17.17 Iye amene akadakomoka, bwenzi lake ayenera kumchitira chifundo;
angaleke kuopa Wamphamvuyonse.
15Abale anga anachita monyenga ngati kamtsinje,
ngati madzi a timitsinje akupitirira.
16Amada chifukwa cha madzi oundana.
M'menemo chipale chofewa chibisika;
17atafikira mafundi, mitsinje iuma;
kukatentha, imwerera m'malo mwao.
18Aulendo akutsata njira yao apatukapo,
akwerera poti see, natayika.
19Aulendo a ku Tema anapenyerera,
makamu a ku Sheba anaiyembekezera.
20Anazimidwa popeza adaikhulupirira;
anafikako, nathedwa nzeru.
21Pakuti tsopano mukhala momwemo;
muona choopsa, muchitapo mantha.
22Ngati ndinati, Mundipatse?
Kapena, Muperekeko kwa ine chuma chanu?
23Kapena, Mundilanditse m'dzanja la mdani?
Kapena, Mundiombole m'dzanja la oopsa?
24Mundilangize, ndipo ndidzakhala chete ine;
mundizindikiritse umo ndinalakwira.
25Mau oongoka si ndiwo amphamvu?
Koma kudzudzula kwanu mudzudzula chiyani?
26Kodi muyesa kudzudzula mau?
Popeza maneno a munthu wodololoka akunga mphepo.
27 Mas. 57.6 Indetu, mugwetsera wamasiye msampha,
mumkumbira bwenzi lanu mbuna.
28Koma tsopano balindani, mundipenyerere;
ndikanena bodza pamaso panu mudzalizindikira.
29Bwererani, ndikupemphani, musandiipsire mlandu;
inde, bwereraninso mlandu wanga ngwolungama.
30Kodi pali chosalungama palilime panga?
Ngati sindizindikire zopanda pake m'kamwa mwanga?
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.