1Ndipo magawidwe a ana a Aroni ndi awa. Ana a Aroni: Nadabu, ndi Abihu, Eleazara, ndi Itamara.
2Num. 3.4Koma Nadabu ndi Abihu anafa, atate wao akali ndi moyo, opanda ana; momwemo Eleazara ndi Itamara anachita ntchito ya nsembe.
3Ndipo Davide pamodzi ndi Zadoki wa ana a Eleazara, ndi Ahimeleki wa ana a Itamara, anawagawa, monga mwa malongosoledwe ao mu utumiki wao.
4Ndipo anapeza kuti amuna aakulu a ana a Eleazara anachuluka, a ana a Itamara anachepa; nawagawa motero: pa ana a Eleazara panali khumi mphambu asanu ndi mmodzi, akulu a nyumba za makolo; ndi pa ana a Itamara, monga mwa nyumba za makolo ao, panali asanu ndi atatu.
5Ndipo anawagawa ndi maere, awa ndi aja; pakuti panali akalonga a malo opatulika, ndi akalonga a kwa Mulungu, a ana a Eleazara ndi a ana a Itamara omwe.
6Ndi Semaya mwana wa Netanele mlembi, ndiye wa Alevi, anawalembera pamaso pa mfumu; ndi akalonga, ndi Zadoki wansembe, ndi Ahimeleki mwana wa Abiyatara, a akulu a nyumba za makolo a ansembe ndi Alevi, anatenga nyumba imodzi ya kholo lake ya Eleazara, ndi imodzi ya Itamara.
7Ndipo maere oyamba anamgwera Yehoyaribu, wachiwiri Yedaya,
8wachitatu Harimu, wachinai Seorimu,
9wachisanu Malikiya, wachisanu ndi chimodzi Miyamini,
10Luk. 1.5wachisanu ndi chiwiri Hakozi, wachisanu ndi chitatu Abiya,
11wachisanu ndi chinai Yesuwa, wakhumi Sekaniya,
12wakhumi ndi chimodzi Eliyasibu, wakhumi ndi chiwiri Yakimu,
13wakhumi ndi chitatu Hupa, wakhumi ndi chinai Yesebeabu,
14wakhumi ndi chisanu Biliga, wakhumi ndi chisanu ndi chimodzi Imeri,
15wakhumi ndi chisanu ndi chiwiri Heziri, wakhumi ndi chisanu ndi chitatu Hapizeze,
16wakhumi ndi chisanu ndi chinai Petahiya, wa makumi awiri Yehezikele,
17wa makumi awiri ndi chimodzi Yakini, wa makumi awiri ndi chiwiri Gamuli,
18wa makumi awiri ndi chitatu Delaya, wa makumi awiri ndi chinai Maaziya.
191Mbi. 9.25Awa ndi malongosoledwe ao mu utumiki wao kulowa m'nyumba ya Yehova, monga mwa chiweruzo adawapatsa Aroni atate wao, monga Yehova Mulungu wa Israele anamlamulira.
20Ndipo wa ana otsala a Levi: wa ana a Amuramu, Subaele; wa ana a Subaele, Yedeiya.
21Wa Rehabiya: wa ana a Rehabiya, mkulu ndi Isiya.
22Wa Aizihara: Selomoti; wa ana a Selomoti, Yahati.
23Ndi wa ana a Hebroni: mkulu ndi Yeriya, wachiwiri Amariya, wachitatu Yahaziele, wachinai Yekameamu.
24Wa ana a Uziyele, Mika; wa ana a Mika, Samiri.
25Mbale wa Mika, Isiya; a ana a Isiya, Zekariya.
26Ana a Merari: Mali ndi Musi; mwana wa Yaziya, Beno.
27Ana a Merari: wa Yaziya, Beno, ndi Sohamu, ndi Zakuri, ndi Ibiri.
28Wa Mali: Eleazara, ndiye wopanda ana.
29Wa Kisi: mwana wa Kisi, Yerameele.
30Ndi ana a Musi: Mali, ndi Edere, ndi Yerimoti. Awa ndi ana a Alevi monga mwa nyumba za makolo ao.
31Awanso anachita maere monga abale ao ana a Aroni, pamaso pa Davide mfumu, ndi Zadoki, ndi Ahimeleki, ndi akulu a nyumba za makolo za ansembe ndi Alevi; mkulu wa nyumba za makolo monga mng'ono wake.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.