YESAYA 18 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

Aneneratu za Etiopiya

1 Ezk. 30.4-5, 9 Ha, dziko lakukupuza mapiko, lili tsidya lija la nyanja za Etiopiya;

2limene litumiza mithenga pamtsinje m'ngalawa zamagumbwa zoyenda m'madzi, ndi kuti, Mukani, inu mithenga yoyenda msangamsanga kumtundu wa anthu aatali ndi osalala, kwa mtundu woopsa chikhalire chao, mtundu umene uyesa dziko ndi kupondereza pansi, umene dziko lake nyanja ziligawa!

3Yes. 5.26Inu nonse akukhala m'dziko lapansi, ndi inu akukhazikika padziko lapansi, potukulidwa chizindikiro pamwamba pa mapiri, mudzaona, ndi polizidwa lipenga mudzamva.

4Pakuti Yehova watero kwa ine, Ine ndidzakhala chete, ndipo ndidzayang'ana mokhala chete, ndipo ndidzayang'ana mokhalamo Ine, monga kuwala kotentha kwa dzuwa, monga mtambo wa mame m'kutentha kwa masika.

5Pakuti masika asanafike, kutatha kuphuka ndi posanduka duwa mphesa yofuna kuthyola, iye adzadzombolera tinthambi ndi chikwakwa, ndi nthambi zotasa adzazichotsa ndi kuzisadza.

6Adzasiyira mbalame zakulusa za m'mapiri ndi zilombo za dziko nthambizo, ndipo mbalame zakulusa zidzakhalapo m'dzinja, ndi zilombo zonse za dziko zidzakhalapo m'malimwe.

7Mas. 72.10; Mala. 1.11Nthawi imeneyo mphatso idzaperekedwa kwa Yehova wa makamu, mtundu wa anthu aatali ndi osalala, yochokera kwa mtundu woopsa chikhalire chao; mtundu umene uyesa dziko ndi kupondereza pansi, umene dziko lake nyanja ziligawa, kumalo a dzina la Yehova wa makamu, phiri la Ziyoni.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help