1
mafumu adzabwera nacho chaufulu kukupatsani.
30Dzudzulani chilombo cha m'bango,
khamu la mphongo ndi ng'ombe za anthu,
yense wakudzigonjera ndi ndalama za siliva;
anabalalitsa mitundu ya anthu ya kukondwera nayo nkhondo.
31 Yes. 19.19, 21; 43.3 Akulu adzafumira ku Ejipito;
Kusi adzafulumira kutambalitsa manja ake kwa Mulungu.
32Imbirani Mulungu, maufumu a dziko lapansi inu;
imbirani Ambuye zomlemekeza.
33Kwa Iye wakuberekeka pamwambamwamba,
oyambira kale lomwe;
taonani; amveketsa liu lake, ndilo liu lamphamvu.
34Vomerezani kuti mphamvu nja Mulungu;
ukulu wake uli pa Israele,
ndi mphamvu yake m'mitambo.
35 Mas. 45.3-4 Inu Mulungu, ndinu woopsa m'malo oyera anu;
Mulungu wa Israele ndiye amene apatsa anthu ake
mphamvu ndi chilimbiko.
Alemekezeke Mulungu.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.