1 TIMOTEO 1 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

Paulo alangiza Timoteo

1 Mac. 9.15 Paulo, mtumwi wa Khristu Yesu monga mwa chilamuliro cha Mulungu Mpulumutsi wathu, ndi cha Khristu Yesu, chiyembekezo chathu:

2Mac. 16.1; Tit. 1.4kwa Timoteo mwana wanga weniweni m'chikhulupiriro: Chisomo, chifundo, mtendere za kwa Mulungu Atate ndi kwa Khristu Yesu Ambuye wathu.

3 Mac. 20.1, 3 Monga ndinakudandaulira iwe utsalire mu Efeso, popita ine ku Masedoniya, nditeronso, kuti ukalamulire ena ajawa asaphunzitse kanthu kena,

41Tim. 4.7kapena asasamale nkhani zachabe, ndi mawerengedwe osalekeza a mafuko a makolo, ndiwo akuutsa mafunso, osati za udindo wa Mulungu umene uli m'chikhulupiriro;

5Aro. 13.8, 10koma chitsirizo cha chilamuliro ndicho chikondi chochokera mu mtima woyera ndi m'chikumbu mtima chokoma ndi chikhulupiriro chosanyenga;

6zimenezo, ena pozilambalala anapatukira kutsata mau opanda pake;

7pofuna kukhala aphunzitsi a malamulo ngakhale sadziwitsa zimene azinena, kapena azilimbikirazi.

8Aro. 7.12Koma mudziwa kuti lamulo ndi labwino, ngati munthu achita nalo monga mwa lamulo,

9Agal. 3.19podziwa ichi, kuti lamulo siliikika kwa munthu wolungama, koma kwa osaweruzika ndi osamvera lamulo, osapembedza, ndi ochimwa, osalemekeza ndi amnyozo, akupha atate ndi akupha amai, akupha anzao,

10achigololo, akuchita zoipa ndi amuna, akuba anthu, amabodza, olumbira zonama, ndipo ngati kuli kena kakutsutsana nacho chiphunzitso cholamitsa;

11Akol. 1.25monga mwa Uthenga Wabwino wa ulemerero wa Mulungu wolemekezeka, umene anandisungitsa ine.

12 Akol. 1.25 Ndimyamika Iye wondipatsa ine mphamvu, ndiye Khristu Yesu, Ambuye wathu, kuti anandiyesa wokhulupirika, nandiika kuutumiki,

13Luk. 23.34; Mac. 8.3ndingakhale kale ndinali wamwano, ndi wolondalonda, ndi wachipongwe; komatu anandichitira chifundo, popeza ndinazichita wosazindikira, wosakhulupirira;

14Aro. 5.20koma chisomo cha Ambuye wathu chidachulukatu pamodzi ndi chikhulupiriro ndi chikondi chili mwa Khristu Yesu.

15Mat. 9.13Mauwa ali okhulupirika ndi oyenera konse kuti awalandire, kuti Khristu Yesu anadza kudziko lapansi kupulumutsa ochimwa; wa iwowa ine ndine woposa;

161Ako. 11.1komatu mwa ichi anandichitira chifundo, kuti mwa ine, woyamba, Yesu Khristu akaonetsere kuleza mtima kwake konse kukhale chitsanzo cha kwa iwo adzakhulupirira pa Iye m'tsogolo kufikira moyo wosatha.

17Ndipo kwa Mfumu yosatha, yosavunda, yosaoneka, Mulungu wa yekha, ukhale ulemu ndi ulemerero, kufikira nthawi za nthawi. Amen.

18 1Tim. 4.14 Lamulo ili ndipereka kwa iwe, mwana wanga Timoteo, kuti, monga mwa zonenera zidakutsogolera iwe kale, ulimbane nayo nkhondo yabwino;

191Tim. 3.9; 6.9ndi kukhala nacho chikhulupiriro ndi chikumbumtima chokoma, chimene ena adachikankha, chikhulupiriro chao chidatayika;

201Ako. 5.5; 2Tim. 4.14a iwo ali Himeneo ndi Aleksandro, amene ndawapereka kwa Satana, kuti aphunzire kusalankhula zamwano.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help