YOBU 16 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

Yobu atonza mabwenziwo kuti mau ao samthandiza, akana kuti sanachimwe, nadziponya kwa Mulungu. Chiyembekezo chake ndi imfa

1Pamenepo Yobu anayankha, nati,

2Ndamva zambiri zotere;

inu nonse ndinu otonthoza mtima mondilemetsa.

3Kodi adzatha mau ouluzika?

Kapena chikuwindula nchiyani kuti uyankha zotere?

4 Mali. 2.15 Inenso ndikadanena monga inu,

moyo wanu ukadakhala m'malo mwa moyo wanga,

ndikadalumikizanitsa mau akutsutsana nanu,

ndi kukupukusirani mutu wanga.

5Koma ndikadakulimbikitsani ndi m'kamwa mwanga,

ndi chitonthozo cha milomo yanga chikadatsitsa chisoni chanu.

6Chinkana ndinena chisoni changa sichitsika;

ndipo ndikaleka, chindichokera nchiyani?

7Koma tsopano wandilemetsa Iye;

mwapasula msonkhano wanga wonse.

8Kundigwira kwanu, ndiko umboni wonditsutsa,

kuonda kwanga kundiukira, kuchita umboni pamaso panga.

9Iye ananding'amba m'kundida kwake, nakwiya nane,

anandikukutira mano;

mdani wanga ananditong'olera maso ake.

10Iwo anandiyasamira pakamwa pao;

anandiomba pama ndi kunditonza;

asonkhana pamodzi kunditsutsa.

11 Yob. 1.15, 17 Mulungu andipereka kwa osulangama,

nandiponya m'manja a oipa.

12Ndinali mkupuma, koma anandithyola;

inde anandigwira pakhosi, nandiphwanya;

nandiimika ndikhale chandamali.

13Eni mauta ake andizinga,

ang'amba impso zanga, osazileka;

natsanulira pansi ndulu yanga.

14Andipasulapasula;

andithamangira ngati wamphamvu.

15Ndadzisokerera chiguduli kukhungu langa.

Ndipo ndaipsa mphamvu yanga m'fumbi.

16Nkhope yanga njodetsedwa ndi kulira misozi,

ndi pa zikope zanga pali mthunzi wa imfa;

17pangakhale palibe chiwawa m'manja mwanga,

ndi pemphero langa ndi loyera.

18Dziko iwe, usakwirire mwazi wanga,

ndi kulira kwanga kusowe popumira.

19 Aro. 1.9 Tsopanonso, taona, mboni yanga ili kumwamba,

ndi nkhoswe yanga ikhala m'mwamba.

20Mabwenzi anga andinyoza;

koma diso langa lilirira misozi kwa Mulungu.

21 Yes. 45.9; Aro. 9.20 Ha? Munthu akadapembedzera mnzake kwa Mulungu,

monga munthu apembedzera mnansi wake!

22 Mlal. 12.5 Pakuti zitafika zaka zowerengeka,

ndidzamuka kunjira imene sindibwererako.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help