MLALIKI 5 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

Malangizo osiyana akuwasamalira anthu m'moyo uno

1 Eks. 3.5; Yes. 1.12-15 Samalira phazi lako popita kunyumba ya Mulungu; pakuti kuyandikira kumvera kupambana kupereka nsembe za zitsiru; pakuti sizizindikira kuti zilikuchimwa.

2Miy. 10.19Usalankhule mwanthuku mtima wako, usafulumire kunena kanthu pamaso pa Mulungu; pakuti Mulungu ali kumwamba, iwe uli pansi; chifukwa chake mau ako akhale owerengeka.

3Pakuti loto lafika mwakuchuluka ntchito; ndipo mau a chitsiru mwakuchuluka maneno.

4Num. 30.2; Mas. 66.13-14Utawinda chiwindo kwa Mulungu, usachedwe kuchichita; pakuti sakondwera ndi zitsiru; chita chomwe unachiwindacho.

5Mac. 5.4Kusawinda kupambana kuwinda osachita.

6Usalole m'kamwa mwako muchimwitse thupi lako; usanene pamaso pa mthenga kuti, Ndinaphophonya; Mulungu akwiyire mau ako chifukwa ninji, naononge ntchito ya manja ako?

7Pakuti monga mu unyinji wa maloto muli zachabe motero mochuluka mau; koma dziopa Mulungu.

8 Mas. 58.11 Ukaona anthu alikutsendereza aumphawi, ndi kuchotsa chilungamo ndi chiweruzo mwachiwawa pa dera lina la dziko, usazizwepo; pakuti mkulu wopambana asamalira; ndipo alipo akulu ena oposa amenewo.

9Phindutu la dziko lipindulira onse; ngakhale mfumu munda umthandiza;

10Wokonda siliva sadzakhuta siliva; ngakhale wokonda chuma sadzakhuta phindu; ichinso ndi chabe.

11Pochuluka katundu, akudyapo achulukanso; nanga apindulira eni ake chiyani, koma kungopenyera ndi maso ao?

12Tulo ta munthu wogwira ntchito ntabwino, ngakhale adya pang'ono ngakhale zambiri; koma kukhuta kwa wolemera sikumgonetsa tulo.

13Pali choipa chovuta ndachiona kunja kuno, ndicho, chuma chilikupweteka eni ake pochikundika;

14koma chumacho chionongeka pomgwera tsoka; ndipo akabala mwana, m'dzanja lake mulibe kanthu.

15Yob. 1.21; 1Tim. 6.7Monga anatuluka m'mimba ya amake, adzabweranso kupita wamaliseche, monga anadza osatenga kanthu pa ntchito zake, kakunyamula m'dzanja lake.

16Ichinso ndi choipa chowawa, chakuti adzangopita monse monga anadza; ndipo wodzisautsa chabe adzaona phindu lanji?

17Inde masiku ake onse amadya mumdima, ndipo zimchulukira chisoni ndi nthenda ndi mkwiyo.

18Taonani, chomwe ine ndapenyera kukoma ndi kuyenera munthu ndiko kudya, ndi kumwa, ndi kukondwera ndi ntchito zake zonse asauka nazo kunja kuno, masiku onse a moyo wake umene Mulungu ampatsa; pokhala gawo lake limeneli.

19Inde yemwe Mulungu wamlemeretsa nampatsa chuma, namninkhanso mphamvu ya kudyapo, ndi kulandira gawo lake ndi kukondwera ndi ntchito zake; umenewu ndiwo mtulo wa Mulungu.

20Pakuti sadzakumbukira masiku a moyo wake kwambiri; chifukwa Mulungu amvomereza m'chimwemwe cha mtima wake.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help