DEUTERONOMO 2 - Buku Lopatulika ndilo Mau a Mulungu

1Pamenepo tinabwerera, ndi kuyenda kunka kuchipululu, kutsata njira ya Nyanja Yofiira, monga Yehova adanena ndi ine; ndipo tinapaza phiri la Seiri masiku ambiri.

2Ndipo Yehova ananena ndi ine, ndi kuti,

3Yakwanira nthawi yakupaza inu phiri ili; tembenukani kunka kumpoto.

4Ndipo uuze anthu, ndi kuti, Mukapite kubzola malire a abale anu, ana a Esau okhala mu Seiri; ndipo adzakuopani; muchenjere ndithu;

5Gen. 36.8musalimbana nao; popeza sindikupatsakoni dziko lao, pangakhale popondapo phazi lanu ai; pakuti ndapatsa Esau phiri la Seiri likhale lakelake.

6Mugulane nao chakudya ndi ndalama, kuti mudye; mugulane naonso madzi kuti mumwe.

7Pakuti Yehova Mulungu wanu anakudalitsani mu ntchito zonse za manja anu; anadziwa kuyenda kwanu m'chipululu ichi chachikulu; zaka izi makumi anai Yehova Mulungu wanu anakhala ndi inu; simunasowe kanthu.

8Potero tinapitirira abale athu, ana a Esau okhala mu Seiri, njira ya chidikha, ku Elati ndi ku Eziyoni-Gebere. Pamenepo tinatembenuka ndi kudzera njira ya chipululu cha Mowabu.

9Ndipo Yehova anati kwa ine, Usavuta Mowabu, kapena kuutsana naye nkhondo; popeza sindidzakupatsako dziko lake likhale lakolako; pakuti ndinapatsa ana a Loti Ari likhale laolao.

10(Aemimu anakhalamo kale, ndiwo anthu aakulu, ndi ambiri, ndi ataliatali, ngati Aanaki.

11Anawayesa iwonso Arefaimu, monga Aanaki; koma Amowabu awatcha Aemimu.

12Ndipo Ahori anakhala mu Seiri kale, koma ana a Esau analanda dziko lao, nawaononga pamaso pao, nakhala m'malo mwao; monga Israele anachitira dziko lakelake, limene Yehova anampatsa).

13Ukani tsopano, olokani mtsinje wa Zeredi. Ndipo tinaoloka mtsinje wa Zeredi.

14Num. 26.64Ndipo masiku amene tinayenda kuchokera ku Kadesi-Baranea, kufikira tidaoloka mtsinje wa Zeredi, ndiwo zaka makumi atatu mphambu zisanu ndi zitatu; kufikira utatha mbadwo wonse wa amuna ankhondo m'chigono, monga Yehova adawalumbirira.

15Komanso dzanja la Yehova linatsutsana nao, kuwaononga m'chigono, kufikira adawatha.

16Ndipo kunali, atatha kufa amuna onse ankhondo mwa anthu,

17Yehova ananena ndi ine, ndi kuti,

18Lero lomwe utumphe malire a Mowabu, ndiwo Ari.

19Ndipo pamene uyandikiza popenyana ndi ana a Amoni, usawavuta, kapena kuutsana nao; popeza sindidzakupatsako dziko la ana a Amoni likhale lakolako; popeza ndinapatsa ana a Loti ili likhale laolao.

20(Ilinso aliyesa dziko la Arefaimu; Arefaimu anakhalamo kale; koma Aamoni awatcha Azamzumimu;

21ndiwo anthu aakulu, ndi ambiri, ndi ataliatali, monga Aanaki; koma Yehova anawaononga pamaso pao; ndipo analanda dziko lao, nakhala m'malo mwao;

22monga Iye anachitira ana a Esau, akukhala mu Seiri, pamene anaononga Ahori pamaso pao; ndipo analanda dziko lao, nakhala m'malo mwao kufikira lero lomwe.

23Kunena za Aavimu akukhala m'midzi kufikira ku Gaza, Akafitori, akufuma ku Kafitori, anawaononga, nakhala m'malo mwao).

24Uka, yenda ulendo wako, ndi kuoloka mtsinje wa Arinoni; taonani, ndapereka Sihoni mfumu ya Hesiboni, Mwamori, ndi dziko lake m'dzanja lako; yamba kulilandira, ndi kuutsana naye nkhondo.

25Tsiku lino ndiyamba kuopsetsa nawe ndi kuchititsa mantha nawe anthu a pansi pa thambo lonse, amene adzamva mbiri yako, nadzanjenjemera, nadzawawidwa chifukwa cha iwe.

26Ndipo ndinatuma amithenga ochokera ku chipululu cha Kedemoti kwa Sihoni mfumu ya Hesiboni ndi mau a mtendere, ndi kuti,

27Num. 21.21-22Ndipitire m'dziko mwako; ndidzatsata mseu, osapatuka ine ku dzanja lamanja kapena kulamanzere,

28Undigulitse chakudya ndi ndalama, kuti ndidye; ndi kundipatsa madzi kwa ndalama, kuti ndimwe; chokhachi ndipitire choyenda pansi;

29monga anandichitira ana a Esau akukhala mu Seiri, ndi Amowabu akukhala mu Ari; kufikira nditaoloka Yordani kulowa dziko limene Yehova Mulungu wathu atipatsa.

30Koma Sihoni mfumu ya Hesiboni sanatilole kupitira kwao; popeza Yehova Mulungu wanu anaumitsa mzimu wake, nalimbitsa mtima wake, kuti ampereke m'dzanja lanu, monga lero lino.

31Ndipo Yehova anati kwa ine, Taona, ndayamba kupereka Sihoni ndi dziko lake pamaso pako; yamba kulandira dziko lake likhale lakolako.

32Pamenepo Sihoni anatuluka kukomana nafe, iye ndi anthu ake onse, kumenyana nafe nkhondo ku Yahazi.

33Ndipo Yehova Mulungu wathu anampereka iye pamaso pathu; ndipo tinamkantha, iye ndi ana ake aamuna ndi anthu ake onse.

34Ndipo muja tinalanda mizinda yake yonse; ndipo tinaononga konse mizinda yonse, amuna ndi akazi ndi ana; sitinasiyapo ndi mmodzi yense.

35Zoweta zokha tinadzifunkhira, pamodzi ndi zofunkha za mizinda tidailanda.

36Mas. 44.3Kuyambira ku Aroere, ndiko kumphepete kwa mtsinje wa Arinoni, ndi kumudzi wokhala kumtsinje kufikira ku Giliyadi, kunalibe mzinda wakutitalikira malinga ake; Yehova Mulungu wathu anapereka yonse pamaso pathu.

37Ku dziko la ana a Amoni lokha simunayandikize; dera lonse la mtsinje wa Yaboki, ndi mizinda ya kumapiri, ndi kwina kulikonse Yehova Mulungu wathu anatiletsa.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help