1 Mlal. 5.13 Pali choipa ndachiona kunja kuno chifalikira mwa anthu,
2Luk. 12.20munthu amene Mulungu wamlemeretsa nampatsa chuma ndi ulemu, mtima wake susowa kanthu kena ka zonse azifuna, koma Mulungu osampatsa mphamvu ya kudyapo, koma mlendo adyazo; ichi ndi chabe ndi nthenda yoipa.
3Mlal. 1.13; Yes. 14.19-20Chinkana munthu akabala ana makumi khumi, nakhala ndi moyo zaka zambiri, masiku a zaka zake ndi kuchuluka, koma mtima wake osakhuta zabwino, ndiponso alibe maliro; nditi, Nsenye iposa ameneyo;
4pakuti ikudza mwachabe, nichoka mumdima, mdima nukwirira dzina lake.
5Ngakhale dzuwa siliona ngakhale kulidziwa, imeneyi ipambana winayo kupuma;
6akakhala ndi moyo zaka zikwi ziwiri, koma osakondwera; kodi onse sapita kumalo amodzi?
7Ntchito zake zonse munthu angogwirira m'kamwa mwake, koma mtima wake sukhuta.
8Pakuti wanzeru ali ndi chiyani choposa chitsiru? Waumphawi wodziwa kuyenda pamaso pa amoyo ali ndi chiyani?
9Kupenya kwa maso kuposa kukhumba kwa mtima; ichinso ndi chabe ndi kungosautsa mtima.
10 Yes. 45.9 Chomwe chinalipo chatchedwa dzina lake kale, chidziwika kuti ndiye munthu; sangathe kulimbana ndi womposa mphamvu.
11Pokhala zinthu zambiri zingochulukitsa zachabe, kodi anthu aona phindu lanji?
12Yak. 4.14Pakuti ndani adziwa chomwe chili chabwino kwa munthu ali ndi moyo masiku onse a moyo wake wachabe umene autsiriza ngati mthunzi? Pakuti ndani adzauza munthu chimene chidzaoneka m'tsogolo mwake kunja kuno?
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.