1Ndipo Yehosafati anagona pamodzi ndi makolo ake, naikidwa pamodzi ndi makolo ake m'mzinda wa Davide; ndi Yehoramu mwana wake anakhala mfumu m'malo mwake.
2Ndipo anali nao abale ake, ana a Yehosafati, Azariya, ndi Yehiyele, ndi Zekariya, ndi Azariya, ndi Mikaele, ndi Sefatiya, onsewa ndiwo ana a Yehosafati mfumu ya Israele.
3Ndipo atate wao anawapatsa mphatso zazikulu, zasiliva, ndi zagolide, ndi za mtengo wake, pamodzi ndi mizinda yamalinga mu Yuda; koma ufumu anauninkha kwa Yehoramu; pakuti ndiye mwana wake woyamba.
4Atauka tsono Yehoramu mu ufumu wa atate wake, nadzilimbitsa, anapha ndi lupanga abale ake onse, ndi akalonga ena omwe a Israele.
52Maf. 8.17-22Yehoramu anali wa zaka makumi atatu mphambu ziwiri polowa ufumu wake, nachita ufumu mu Yerusalemu zaka zisanu ndi zitatu.
6Nayenda m'njira ya mafumu a Israele, umo mwana wamkazi wa Ahabu anali mkazi wake; ndipo anachita choipa pamaso pa Yehova.
7Koma Yehova sanafune kuononga nyumba ya Davide chifukwa cha pangano adalichita ndi Davide, ndi monga adalonjeza kumpatsa iye ndi ana ake nyali nthawi zonse.
8Masiku ake Aedomu anapanduka kuchoka m'dzanja la Yuda, nadziponyera okha mfumu.
9Ndipo Yehoramu anaoloka, ndi akazembe ake, ndi magaleta ake onse pamodzi naye, nauka usiku, nakantha Aedomu omzinga ndi akapitao a magaleta.
10Chinkana anatero, Aedomu anapanduka kupulumuka m'dzanja la Yuda mpaka lero lino; nthawi yomweyo anapanduka Alibina kupulumuka m'dzanja lake; chifukwa adasiya Yehova Mulungu wa makolo ake.
11Anamanganso misanje m'mapiri a Yuda, nachititsa okhala mu Yerusalemu chigololo, nakankhirako Ayuda.
12Ndipo anamdzera kalata yofuma kwa Eliya mneneri, ndi kuti, Atero Yehova Mulungu wa Davide atate wanu, Popeza simunayende m'njira za Yehosafati atate wanu, kapena m'njira za Asa mfumu ya Yuda,
131Maf. 16.31-33koma mwayenda m'njira ya mafumu a Israele, ndi kuchititsa Yuda ndi okhala mu Yerusalemu chigololo, monga umo anachitira chigololo a nyumba ya Ahabu, mwaphanso abale anu a nyumba ya atate wanu, ndiwo abwino akuposa inu;
14taonani, Yehova adzakantha anthu anu, ndi ana anu, ndi akazi anu, ndi chuma chanu chonse, makanthidwe aakulu;
15ndipo mudzadwala kwakukulu nthenda yamatumbo, mpaka matumbo anu adzatuluka chifukwa cha nthendayi tsiku ndi tsiku.
161Maf. 11.14, 23Ndipo Yehova anautsira Yehoramu mzimu wa Afilisti, ndi wa Aarabu okhala pambali pa Akusi;
17ndiwo anakwerera Yuda, nathyolamo, nalanda chuma chonse chinapezeka m'nyumba ya mfumu, ndi ana ake omwe, ndi akazi ake, osamsiyira mwana, koma Ahaziya yekha mwana wake wamng'ono.
18Ndi pambuyo pake pa izi zonse Yehova anamdwalitsa m'matumbo ake ndi nthenda yosachira nayo.
19Ndipo kunali, itapita nthawi, pakutha pake pa zaka ziwiri, anatuluka matumbo ake mwa nthenda yake namwalira nazo nthenda zoipa. Ndipo anthu ake sanampserezere zonunkhira, monga umo anapserezera makolo ake.
20Anali wa zaka makumi atatu mphambu ziwiri polowa ufumu wake, nakhala mfumu mu Yerusalemu zaka zisanu ndi zitatu, namuka wopanda wina womlakalaka; ndipo anamuika m'mzinda wa Davide, koma si m'manda a mafumu ai.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.